1 Ezek. 47.1; Zek. 14.8 Pambuyo pake mngelo uja adandiwonetsa mtsinje wa madzi opatsa moyo. Mtsinjewo madzi ake anali onyezimira ngati galasi, ndipo unkachokera ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja.
2Gen. 2.9; 2Es. 2.12; 7.123 Unkayenda pakati pa mseu wamumzinda uja. Pa mbali zonse ziŵiri za mtsinje panali mtengo wopatsa moyo. Mtengowo umabala zipatso khumi ndi kaŵiri pa chaka, kamodzi mwezi uliwonse, ndipo masamba ake ndi ochiritsa anthu a mitundu yonse.
3Zek. 14.11; Gen. 3.17Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza.
42Es. 7.98Iwo azidzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala lolembedwa pamphumi pao.
5Yes. 60.19; Dan. 7.18Sikudzakhalanso usiku, ndipo sipadzafunikanso kuŵala kwa nyale kapena kuŵala kwa dzuŵa, pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuŵala kwake, ndipo iwo adzakhala mafumu olamulira mpaka muyaya.
Za kubwera kwake kwa Yesu6Pambuyo pake mngelo uja adandiwuza kuti, “Mau aŵa ndi oona ndiponso oyenera kuŵakhulupirira. Ndipo Ambuye Mulungu amene amalankhulitsa aneneri, adatuma mngelo wao kuti aonetse atumiki ao zimene zidzachitike posachedwa.”
7Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ngwodala munthu amene amatsata mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo.”
8Ndine, Yohane, amene ndidamva ndi kuwona zimenezi. Ndipo nditazimva ndi kuziwona, ndidadzigwetsa ku mapazi a mngelo uja amene adandiwonetsa zimenezi. Ndidaati ndimpembedze,
9koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ngati abale ako aneneri, ndiponso ngati onse otsata mau olembedwa m'buku lino. Iwe pembedza Mulungu.”
10Adandiwuzanso kuti, “Usabise mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo, pakuti nthaŵi yake ili pafupi.
11Dan. 12.10Wochita zoipa apitirire kuchita zoipazo, ndipo wodetsedwa ndi zonyansa apitirire kudzidetsa ndi zonyansazo. Wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo, ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”
12 Yes. 40.10; 62.11; Mas. 28.4; Yes. 40.10; Yer. 17.10 Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita.
13Chiv. 1.8; Yes. 44.6; 48.12; Chiv. 1.17; 2.8Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimalizo ndine.”
14 Gen. 2.9; 3.22 Ngodala amene amachapa mikanjo yao, kuti aloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyo, ndiponso kuloŵa mu mzinda kudzera pa zipata zija.
15Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.
16 Yes. 11.1, 10 “Ine, Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti akufotokozereni zimenezi ndipo zithandize mipingo. Ine ndine chiphukira chotuluka mwa mfumu Davide, ndine chidzukulu chake. Ndine Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa!”
17 Yes. 55.1 Mzimu Woyera ndi Mkwati wamkazi akuti, “Bwerani!” Aliyense womva mauŵa, anenenso kuti, “Bwerani!” Aliyense womva ludzu, abwere. Aliyense woŵafuna, aŵalandire mwaulere madzi opatsa moyo.
Mau otsiriza18 Deut. 4.2; 12.32 Ine Yohane, ndikuchenjeza aliyense womva mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo. Wina akadzaonjezerapo kanthu pa mau ameneŵa, Mulungu adzamuwonjezera miliri ija yalembedwa m'buku munoyi.
19Ndipo wina akadzachotsapo kanthu pa mau a m'buku lino loneneratu zam'tsogolo, Mulungu adzamchotsera gawo lake la zipatso za mtengo wopatsa moyo uja, ndi malo ake omwe mu Mzinda Woyera uja, monga zalembedwera m'buku muno.
20Amene akufotokoza zimenezi akuti, “Indedi, ndikubwera posachedwa.”
Inde, bwerani, Ambuye Yesu.
21Ambuye Yesu akukomereni mtima nonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.