1Yesu adalankhulanso ndi anthu aja m'mafanizo. Adati,
2“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Mfumu ina idaakonzera mwana wake phwando laukwati.
3Idatuma antchito ake kuti akaŵauze anthu amene adaaitanidwa kuphwandoko kuti azibwera, anthuwo nkukana.
4Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’
5Koma oitanidwawo sadalabadireko, adangopita ku zao: wina kumunda kwake, wina ku ntchito yake yamalonda.
6Enawo adagwira antchito a mfumu aja naŵazunza, nkuŵapha.
7“Pamenepo mfumu idapsa mtima kwambiri, mwakuti idatuma ankhondo ake kuti akaononge opha anzao aja, ndi kutentha mudzi wao.
8Pambuyo pake idauza antchito ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzekatu, koma oitanidwa aja anali osayenera.
9Pitani tsono ku mphambano za miseu, mukaitane aliyense amene mukampeze, kuti abwere kuno ku phwando laukwati.’
10Apo antchitowo adapitadi ku miseu nakasonkhanitsa onse amene adaŵapeza, abwino ndi oipa omwe, mwakuti nyumba yaphwando idadzaza ndi anthu.
11“Pamene mfumu ija idaloŵa m'nyumbamo kukaona anthu odzadya phwando aja, idapezamo wina amene sadavale chovala chaukwati.
12Tsono idamufunsa kuti ‘Kodi iwe, waloŵa bwanji muno opanda chovala chaukwati?’ Iye uja adangoti chete.
13Mt. 8.12; 25.30; Lk. 13.28Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, ‘Mmangeni manja ndi miyendo, mukamponye kunja ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.’ ”
14 2Es. 8.3 Tsono Yesu adati, “Inde oitanidwa ngambiri, komatu osankhidwa ngoŵerengeka.”
Za kukhoma msonkho(Mk. 12.13-17; Lk. 20.20-26)15Nthaŵi ina Afarisi adakapangana zodzatapa Yesu m'kamwa.
16Adatuma ophunzira ao ena pamodzi ndi ena a m'chipani cha Herode kwa Yesu. Iwoŵa adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Paja Inu simuyang'anira kuti uyu ndani.
17Ndiye timati mutiwuze zimene mukuganiza. Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?”
18Koma Yesu podziŵa maganizo ao oipa, adati, “Bwanji kodi mukundiyesa dala, anthu achiphamasonu?
19Tandiwonetsani ndalama yamsonkho.” Iwo adampatsadi ndalamayo.
20Pamenepo Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?”
21Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.”
22Atamva zimenezi, anthuwo adathedwa nzeru, motero adamsiya nachokapo.
Za kuuka kwa akufa(Mk. 12.18-27; Lk. 20.27-40)23 Ntc. 23.8 Tsiku lomwelo Asaduki ena adadza kwa Yesu. (Paja iwo amati akufa sadzauka.) Adamufunsa kuti,
24Deut. 25.5 “Aphunzitsi, Mose adati, ‘Ngati munthu amwalira opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’
25Tsono kwathu kudaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, nkumwalira. Tsono popeza kuti analibe mwana, adasiyira mbale wake mkazi wake uja.
26Chimodzimodzinso wachiŵiri ndi wachitatu, mpaka wachisanu ndi chiŵiri.
27Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira.
28Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti pakati pa abale asanu ndi aŵiri aja, popeza kuti onsewo adaamkwatirapo?”
29Yesu adaŵayankha kuti, “Mukulakwa chifukwa simudziŵa Malembo, ngakhalenso mphamvu za Mulungu.
30Lun. 5.5Pajatu pouka akufa, palibenso za kukwatira kapena kukwatiwa ai. Onse ali ngati angelo Kumwamba.
31Tsono zakuti anthu adzauka kwa akufa, kodi simudaŵerenge zimene Mulungu adakuuzani zija kuti,
32Eks. 3.6 ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndine Mulungu wa Isaki, ndine Mulungu wa Yakobe?’ Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo.”
33Pamene anthu ochuluka aja amene anali pamenepo adamva zimenezi, adadabwa kwambiri ndi zophunzitsa zake.
Za lamulo lalikulu(Mk. 12.28-34; Lk. 10.25-28)34Afarisi atamva kuti Yesu adatsutsa Asaduki, adasonkhana.
35Tsono mmodzi mwa iwo, katswiri wa Malamulo, adafunsa Yesu funso kuti amutape m'kamwa.
36Adati, “Aphunzitsi, kodi mwa malamulo onse a Mulungu, lalikulu ndi liti?”
37Deut. 6.5 Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.
38Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu.
39Lev. 19.18 Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
40Lk. 10.25-28Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.”
Za Mpulumutsi wolonjezedwa uja(Mk. 12.35-37; Lk. 20.41-44)41Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu adaŵafunsa funso.
42Adati, “Mumaganiza chiyani za Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Mumati ndi mwana wa yani?” Iwo aja adati, “Ndi mwana wa Davide.”
43Iye adaŵafunsa kuti, “Tsono bwanji nanga Davideyo ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera, akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake? Paja adati,
44 Mas. 110.1 “ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti,
Khala ku dzanja langa lamanja,
mpaka nditasandutsa adani ako
kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’
45“Ngati Davide akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake, angakhale mwana wakenso bwanji?”
46Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumuyankha ngakhale mau amodzi. Tsono kuyambira tsiku limenelo panalibenso munthu amene adalimba mtima kuti amufunse mafunso.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.