Yer. 36 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Baruki aŵerenga buku m'Nyumba ya Mulungu

1 2Maf. 24.1; 2Mbi. 36.5-7; Dan. 1.1, 2 Chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, Chauta adauza Yeremiya kuti,

2“Tenga buku ndipo ulembepo mau onse amene ndalankhula nawe za Israele ndi Yuda ndi za mitundu yonse ya anthu, kuyambira tsiku limene ndidalankhula nawe nthaŵi ya Yosiya mpaka lero lino.

3Mwina mwake banja la Yuda lidzamva za zoopsa zonse zimene ndikuti ndiŵagwetsere. Choncho munthu aliyense adzasiya makhalidwe ake oipa. Motero ndidzaŵakhululukira zolakwa zao ndi machimo ao.”

4Tsono Yeremiya adaitana Baruki mwana wa Neriya. Ndipo Barukiyo adalemba m'bukumo mau onse amene Yeremiya ankamuuza, ndiye kuti mau onse amene Chauta adalankhula ndi Yeremiyayo.

5Adauza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Chauta.

6Ndiye tsono upite ndiwe kumeneko m'malo mwanga pa tsiku losala chakudya, ukaŵerenge mau a Chauta amene ndidakulembetsa m'bukumu, anthu onse alikumva. Udzaŵaŵerenge kwa anthu onse a ku Yuda amene abwera kuchokera ku mizinda yao.

7Tsono mwina mwake adzapemba kwa Chauta, ndipo munthu aliyense adzasiya makhalidwe ake oipa. Ndithu Chauta waŵakwiyira anthu ameneŵa, ukali wake ndi woyaka kwabasi.”

8Motero Baruki mwana wa Neriya adachita zonse zimene mneneri Yeremiya adamuuza kuti achite. Adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja m'Nyumba ya Chauta.

9Pa mwezi wachisanu ndi chinai wa chaka chachisanu cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, anthu onse a ku Yerusalemu ndi onse amene adaabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, adapangana za kusala chakudya kuti apepese Chauta.

10Tsono onse ataloŵa m'Nyumba ya Chauta, Baruki adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja, anthu onse alikumva. Adaŵerengera m'chipinda cha Gemariya, mwana wa mlembi Safani, chimene chinali m'bwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano choloŵera ku Nyumba ya Chauta.

Aŵerenga buku pamaso pa akuluakulu

11Mikaya mwana wa Gemariya, mdzukulu wa Safani, atamva mau onse a Chauta olembedwa m'buku aja,

12adapita ku nyumba ya mfumu, nakaloŵa m'chipinda cha mlembi. Akuluakulu onse anali atasonkhana m'menemo: mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akobori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena onse.

13Tsono Mikaya adaŵauza mau onse amene adamva pamene Baruki ankaŵerenga buku anthu alikumva.

14Pamenepo akuluakulu adatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuuza kuti abwere nalo buku limene ankaŵerengera anthu. Motero Baruki mwana wa Neriya, adapita nalo bukulo kwa iwo.

15Iwowo adati, “Khala apa, ndipo utiŵerengere.” Baruki adaŵaŵerengeradi.

16Atamva zimene adaaŵerengazo, adayamba kuyang'anitsitsana ali njenjenje ndi mantha. Tsono adauza Baruki kuti, “Tiyenera kuŵauza amfumu mau onseŵa.

17Koma tatiwuza, m'mene udalembera mau onseŵa. Kodi ndi Yeremiya adakulembetsa zimenezitu ati?”

18Baruki adayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiyadi amene ankanditchulira mau ameneŵa, ine nkumalemba ndi inki m'buku.”

19Akuluakulu aja adauza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiyayo mukabisale, pasakhale munthu wodziŵa kumene muli.”

Mfumu itentha Bukulo

20Tsono iwo adaloŵa m'bwalo napita kwa mfumu ataika bukulo m'chipinda cha mlembi Elisama. Adaiwuza mfumuyo mau onsewo.

21Mfumu itamva zimenezi, idatuma Yehudi kukatenga buku lija. Atakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama, Yehudi adaŵerengera mfumu ndi akuluakulu onse amene adasonkhana.

22Unali mwezi wachisanu ndi chinai ndipo mfumu inali m'nyumba ya pa nyengo yachisanu, ikuwotha moto umene ankasonkha chifukwa cha kuzizira.

23Yehudi ankati akaŵerenga masamba atatu kapena anai a bukulo, mfumu inkaŵagwira nkuŵadula ndi mpeni, niŵaponya m'malaŵi a moto. Idapitirira kuchita zimenezi mpaka buku lonse lidapsa ndi moto.

24Komabe mfumu kapena wina aliyense mwa aphungu ake amene adamva mau ameneŵa, sadachite mantha kapena kung'amba zovala zao.

25Ndipo pamene Elinatani, Delaya ndi Gemariya adapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, iyoyo sidaŵamvere.

26Kenaka mfumu idalamula Yerahamele mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Aziriele ndi Selemiya mwana wa Abideele kuti akagwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma Chauta anali ataŵabisa.

Yeremiya alemba buku lina

27Tsono mfumu itatentha bukulo m'mene munali zonse zimene Yeremiya adaalembetsa Baruki, Chauta adauza Yeremiya kuti,

28“Tsopano tenga buku lina kuti ulembemo mau onse amene adaali m'buku loyamba, limene Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, adatentha.

29Ndipo za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, ukamuuze kuti, ‘Chauta akuti, Paja iwe udatentha buku lija, nkumanena kuti, “Chifukwa chiyani walemba kuti mfumu ya ku Babiloni idzafika kudzaononga dziko lino ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe?”

30Nchifukwa chake za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, Chauta akunena kuti sipadzaoneka wina woloŵa m'malo mwake pa mpando waufumu wa Davide. Akadzafa, mtembo wake masana udzakhala pa dzuŵa, ndipo usiku udzakhala pa chisanu.

31Ndidzamlanga pamodzi ndi zidzukulu zake ndi aphungu ake chifukwa cha zoipa zao. Ndidzaŵagwetsera iwowo ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda zoopsa zonse zimene ndidanena, chifukwa iwo sadamvere mau anga.’ ”

32Tsono Yeremiya adatenga buku lina napatsa mlembi Baruki, mwana wa Neriya, namlembetsa mau onse a m'buku limene Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda adatentha lija. Ndipo adaonjezerapo mau ambiri monga omwewo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help