1Ndiyenera kunyada, tsono kunyada kwake nkopanda phindu. Komabe ndimati ndikambe za zimene Ambuye adandiwonetsa m'masomphenya, ndiponso za zimene adandiwululira.
2Ndikudziŵa mkhristu wina amene adaatengedwa mwadzidzidzi kupita Kumwambamwamba. Papita zaka khumi ndi zinai chichitikire cha zimenezi. Sindidziŵa ngati zidaachitika ali m'thupi kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi.
3Ndikudziŵa kuti munthuyo adaatengedwa mwadzidzidzi kupita ku Paradizo. Sindikudziŵa ngati zimenezi zidaachitika ali m'thupi, kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi.
4Kumeneko munthuyo adamva zinthu zosasimbika, zinthu zimene munthu sangazilankhule.
5Munthu wotere ndidzamnyadira, koma kunena za ine ndekha, sindidzanyadira kanthu kena koma kufooka kwanga kokha.
6Ndikadafuna kunyada, sindikadakhala ngati wopusa, chifukwa ndikadalankhula zoona zokha. Koma sindidzanyada, kuwopa kuti wina aliyense angandiyese wopambana, kusiyana ndi m'mene amandiwonera, ndiponso ndi m'mene amandimvera ndikamalankhula.
7Koma kuwopa kuti ndingamadzitukumule chifukwa cha zazikulu kwambiri zimene Ambuye adandiwululira, Mulungu adandipatsa cholasa ngati minga m'thupi. Adalola wamthenga wa Satana kuti azindimenya, kuti ndingamanyade kwambiri.
8Pamenepo ndidapempha Ambuye katatu kuti andichotsere chimenechi,
9koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
10Tsono ndimakondwera pamene ndili wofooka, pamene anthu andinyoza, namandizunza, ndiponso pamene ndimva zoŵaŵa ndi kusautsidwa chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, mpamene ndili ndi mphamvu.
Za nkhaŵa ya Paulo chifukwa cha mpingo wa ku Korinto11Ndasanduka wopusa, koma ndinu mwandichititsa zimenezi. Ndinu mukadayenera kundichitira umboni. Pakuti ngakhale sindili kanthu, atumwi anu apamwamba aja sandipambana pa kanthu kalikonse.
12Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu.
13Kodi nchiyani chimene ndidachitira mipingo ina, inu osakuchitirani, kupatula chokhachi chakuti sindidakhale ngati katundu wokulemetsani? Ndikhululukireni kulakwa kwangaku.
14Aka nkachitatu tsopano kukonzeka kuti ndibwere kwanuko, ndipo sindidzakhala ngati katundu wokulemetsani. Sindikufuna zinthu zanu, koma ndikufuna inuyo. Pakuti si udindo wa ana kusungira makolo ao chuma, koma ndi udindo wa makolo kusungira ana ao chuma.
15Kunena za ine, ndidzakondwa kupereka zanga zonse, ndi kutaya ngakhale moyo wanga womwe chifukwa cha inu. Ine ndikamakukondani kwambiri chotere, kodi ndiye kuti inuyo muzingondikonda pang'ono?
16Momwemo tsono, mudzandivomereza kuti ine sindidakhale ngati katundu wokulemetsani. Koma kapena wina adzati popeza kuti ndine wochenjera, ndidakuchenjeretsani.
17Kodi kapena ndidakuchenjererani mwa aliyense amene ndidamtuma kwa inu?
18Ndidapempha Tito kuti apite, kenaka ndidatuma mbale wathu wina pamodzi naye. Kodi Titoyo adakuchenjererani? Kodi suja iye ndi ine tinkachita zonse ndi mtima umodzi? Suja tinkatsata njira imodzimodzi?
19Kapena mwakhala mukuganiza kuti tikuyesa kudziteteza pamaso panu. Iyai, koma pokhala pamaso pa Mulungu, timalankhula mwa Khristu, ndipo pa zonsezi, okondedwa anga, timangofuna kukulimbitsani mtima.
20Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo.
21Ndikuwopa kuti ndikadzabweranso kwanuko, mwina Mulungu wanga nkudzandinyazitsa pamaso panu, ineyo nkudzalira misozi chifukwa cha ambiri amene adachimwa kale, ndipo sadalape zonyansa zao, dama lao, ndi mayendedwe ao oipa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.