Eks. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za malamulo a kulipira mlandu

1“Munthu akaba ng'ombe kapena nkhosa, nkuipha kapena kuigulitsa, alipire ng'ombe zisanu pa ng'ombe imodzi, kapena nkhosa zinai pa nkhosa imodzi.

2“Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo.

3Koma ikaphedwa dzuŵa litatuluka, apo padzakhala kulipsira magazi. Pajatu wakuba aliyense ayenera kulipira ndithu. Ngati mbala igwidwa, ndipo ilephera kulipira mlandu, aigulitse chifukwa cha kubako.

4Ngati chinthu yabacho chipezeka chamoyo m'manja mwake, kaya ndi ng'ombe, kaya ndi bulu, kaya ndi nkhosa, mbalayo ilipire moŵirikiza.

5“Munthu akamalekerera zoŵeta zake kuloŵa m'munda mwa munthu wina ndi kukadya mbeu za m'mundamo, mwini zoŵetayo alipire mbeu zabwino kwambiri za m'munda mwake, kapena mphesa zake zabwino kwambiri.

6“Moto ukabuka mpaka kukafika ku thengo, ndipo ukatentha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula kapena munda umene uli ndi mbeu, amene adatenthayo alipire zoonongekazo.

7“Munthu akasungiza mnzake ndalama kapena zina zamtengowapatali, ndipo zibedwa m'nyumba mwa munthumo, mbalayo ilipire moŵirikiza.

8Mbalayo ikapanda kupezeka, mwini nyumba uja atengedwe ndi kufika naye pamaso pa Mulungu, kuti ziwoneke ngati katunduyo sadatenge ndi iyeyo.

9“Pakakhala mkangano wina uliwonse pa za chinthu cha mwiniwake kaya ndi ng'ombe, bulu, nkhosa, zovala kapena china chilichonse chotayika, chimene wina akuti nchake, anthu aŵiriwo abwere nawo pamaso pa Mulungu. Amene Mulungu ampeze kuti ndiye wolakwa, adzalipira mnzakeyo moŵirikiza.

10“Munthu akapereka ng'ombe, nkhosa kapena choŵeta chilichonse kwa munthu wina kuti amsungire, tsono choŵeta chija nkufa, kapena kupweteka kapena kutengedwa, wina osaona,

11zitsimikizike pakulumbiritsa wosungayo pamaso pa Chauta kuti sadatenge chamwinicho. Ngati sichidabedwe, mwini wakeyo adzangoti zagwa zatha, ndipo wosungayo asalipire.

12Koma ngati choŵetacho chidabedwa, mwiniwakeyo adzalipidwa.

13Ngati chidajiwa ndi zilombo, atengeko zotsalira zake kuti zikhale mboni, koma asalipire chimene chidajiwa ndi zilombocho.

14“Munthu akabwereka choŵeta kwa mnzake, tsono choŵeta chija nkupweteka mpaka kufa pamene sichili kwa mwiniwakeyo, wobwerekayo alipire ndithu choŵetacho.

15Koma ngati chili kwa mwiniwakeyo, wobwereka uja asalipire. Choŵetacho akachibwereka, tsono nkuwonongeka, mtengo wolipira pobwereka ndiwo udzakonze mlanduwo.

Malamulo a kakhalidwe ka anthu ndi a chipembedzo

16 Deut. 22.28, 29 “Munthu akanyenga namwali wosadziŵa mwamuna, yemwe sanatomeredwe, nagona naye, alipire chiwongo, ndipo amkwatire.

17Koma ngati bambo wake wa namwaliyo akana kuti mwana wakeyo asakwatiwe, munthuyo adzangolipirabe ndalama za chiwongo cha namwali.

18 Deut. 18.10, 11 “Munthu wamkazi wochita zaufiti, musamlole kuti akhale moyo.

19 Lev. 18.23; 20.15, 16; Deut. 27.21 “Aliyense wogona ndi nyama aphedwe basi.

20 Deut. 17.2-7 “Aliyense wopereka nsembe kwa milungu, osati kwa Chauta yekha, aphedwe ameneyo.

21 Eks. 23.9; Lev. 19.33, 34; Deut. 24.17, 18; 27.19 “Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito.

22Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.

23Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine.

24Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye.

25 Lev. 25.35-38; Deut. 15.7-11; 23.19, 20 “Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja.

26Deut. 24.10-13 Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe,

27poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo.

28 Ntc. 23.5 “Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu.

29“Musachedwe kundipatsa zopereka zotapa pa zokolola zanu zambiri ndiponso pa vinyo wanu wochuluka.

“Mundipatse ana anu achisamba aamuna.

30Mundipatsenso ana oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwayo adzangokhala ndi mai wake masiku asanu ndi aŵiri, ndipo mudzampereka kwa Ine pa tsiku lachisanu ndi chitatu.

31 Lev. 17.15 “Mudzakhale anthu operekedwa kwa Ine. Motero musadzadye nyama ya choŵeta chilichonse chojiwa ndi zilombo ku thengo. Nyama imeneyo mudzapatse agalu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help