1 Mbi. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide agwira Raba(2 Sam. 12.26-31)

1 2Sam. 11.1 Itayamba nthaŵi ya phukira chaka chotsatira, nthaŵi imene mafumu ankapita kukamenya nkhondo, Yowabu adatsogolera gulu lankhondo, nakaononga dziko la Aamoni, kenaka adapita kuti akazinge mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu. Tsono Yowabu adakantha mzinda wa Raba naugwetsa.

2Davide adaivula chisoti chagolide mfumu yao, ndipo atachiyesa, adapeza kuti chinkalemera makilogramu 5, ndipo pachisotipo panali mwala wamtengowapatali. Davide adachivala chisoticho, natenga zofunkha zochuluka mumzindamo.

3Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo, zikumbiro zachitsulo ndi nkhwangwa. Umu ndimo m'mene Davide adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davideyo adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse.

Davide amenyana ndi Afilisti(2 Sam. 21.15-22)

4Zitapita zimenezi, padauka nkhondo pakati pa Aisraele ndi Afilisti ku Gezere. Tsono Sibekai Muhusati adapha Sipai amene anali mmodzi mwa zidzukulu za ziphona zija zotchedwa Arefaimu, ndipo Afilisti adagonjetsedwa.

51Sam. 17.4-7 Kenaka padaukanso nkhondo ndi Afilisti. Tsono Elihanani, mwana wa Yairi, adapha Lami, mbale wa Goliyati Mgiti, amene thunthu la mkondo wake linali lalikulu ngati mtanda woombera nsalu.

6Panalinso nkhondo ku Gati kumene kunali munthu wina wamtali, wa zala zakumanja uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zakumwendonso uku zisanu nndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zonse pamodzi zala 24. Iyeyonso anali mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu.

7Tsiku lina pamene adanyoza Aisraele, Yonatani, mwana wa Simea, mbale wake wa Davide, adamupha.

8Anthuwo anali zidzukulu za Arefaimu a ku Gati, ndipo adaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help