Mt. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zophunzitsa Zapaphiri

1Yesu poona chikhamu cha anthu chija, adakwera pa phiri. Iye atakakhala pansi, ophunzira ake adamtsatira pomwepo.

2Kenaka adayamba kuŵaphunzitsa, adati,

Za anthu odala(Lk. 6.20-23)

3“Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao,

pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.

4 Yes. 61.2 Ngodala anthu amene akumva chisoni,

pakuti Mulungu adzaŵasangalatsa.

5 Mas. 37.11 Ngodala anthu ofatsa,

pakuti Mulungu adzaŵapatsa dziko la pansi pano

kuti likhale lao.

6 Yes. 55.1, 2; Mphu. 24.21 Ngodala anthu amene akumva njala

ndi ludzu lofuna chilungamo,

pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.

7Ngodala anthu ochitira anzao chifundo,

pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo.

8 Mas. 24.3, 4; 2Es. 7.98 Ngodala anthu oyera mtima,

pakuti adzaona Mulungu.

9Ngodala anthu odzetsa mtendere,

pakuti Mulungu adzaŵatcha ana ake.

10 1Pet. 3.14 Ngodala anthu ozunzidwa

chifukwa cha kuchita chilungamo,

pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.

11 1Pet. 4.14 “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine.

122Mbi. 36.16; Mphu. 2.8; Ntc. 7.52Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.

Za mchere ndi kuŵala(Mk. 9.50; Lk. 14.34-35)

13 Mk. 9.50; Lk. 14.34, 35 “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito mpang'ono pomwe, koma kungoutaya kunja basi, anthu nkumauponda.

14 Yoh. 8.12; 9.5 “Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike.

15Mk. 4.21; Lk. 8.16; 11.33Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo.

161Pet. 2.12Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Za Malamulo a Mose(Lk. 16.17)

17“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni.

18Lk. 16.17Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.

19Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.

20Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa aphunzitsi a Malamulo ndi kwa Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.

Za kukwiya(Lk. 12.57-59)

21 Eks. 20.13; Deut. 5.17 “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usaphe. Aliyense wopha mnzake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu,’

22Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.

23“Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu,

24siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija.

25“Uziyanjana msanga ndi mnzako wamlandu, mukali pa njira yopita ku bwalo lamilandu, kuwopa kuti angakakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende.

26Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse.

Za chigololo(Mt. 18.8-9; Mk. 9.43-48)

27 Eks. 20.14; Deut. 5.18 “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usachite chigololo.’

28Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.

29Mt. 18.9; Mk. 9.47Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena.

30Mt. 18.8; Mk. 9.43Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.”

Za kusudzulana(Mt. 19.9; Mk. 10.11-12; Lk. 16.18)

31 Deut. 24.1-4; Mt. 19.7; Mk. 10.4 “Anthu akale aja adaaŵalamulanso kuti, ‘Ngati munthu asudzula mkazi wake, ampatse mkaziyo kalata yachisudzulo.’

32Mt. 19.9; Mk. 10.11, 12; Lk. 16.18; 1Ako. 7.10, 11Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.

Za kulumbira

33 Lev. 19.12; Num. 30.2; Deut. 23.21 “Mudamvanso kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usalumbire monama, koma uchitedi zimene udaŵalonjeza Ambuye molumbira.’

34Yak. 5.12; Yes. 66.1; Mt. 23.22Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muleke nkulumbira komwe. Usalumbire kuti, ‘Kumwambadi!’ Paja Kumwamba kuli mpando waufumu wa Mulungu.

35Yes. 66.1; Mas. 48.2Usalumbire kuti, ‘Pali dziko lapansi!’ Paja dziko lapansi ndi chopondapo mapazi ake. Usalumbire kuti, ‘Pali Yerusalemu!’ Paja Yerusalemu ndi mzinda wa Mfumu yaikulu.

36Usalumbire ngakhale pa mutu wako, pakuti sungathe kusandulitsa ndi tsitsi limodzi lomwe kuti likhale loyera kapena lakuda.

37Muzingoti, ‘Inde,’ kapena ‘Ai.’ Zimene muwonjezerepo nzochokera kwa Satana, Woipa uja.

Za kubwezera choipa(Lk. 6.29-30)

38 Eks. 21.24; Lev. 24.20; Deut. 19.21 “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Diso kulipa diso, dzino kulipa dzino.’

39Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso.

40Munthu akakuzenga mlandu nafuna kukulanda mkanjo wako, umlole atengenso ndi mwinjiro wako womwe.

41Munthu akakukakamiza kuyenda naye mtunda umodzi, uyende naye mitunda iŵiri.

42Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”

Za kukonda adani(Lk. 6.27-28, 32-36)

43 Mphu. 12.4-7 “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Ukonde mnzako, ndi kudana ndi mdani wako.’

44Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.

45Mphu. 4.10Mukatero mudzakhaladi ana a Atate anu amene ali Kumwamba. Paja Iwo amaŵalitsa dzuŵa lao pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.

46Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungalandire mphotho yanji? Kodi suja ngakhale okhometsa msonkho amachita chimodzimodzi?

47Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okha, mwachitapo chiyani pamenepo choposa ena? Kodi suja ngakhale akunja amachita chimodzimodzi?

48Lev. 19.2; Deut. 18.13Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help