1Chaka cha 14 cha ufumu wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya adathira nkhondo mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, nailanda.
2Pambuyo pake mfumu ya ku Asiriyayo idatuma kazembe wake wankhondo kuchokera ku Lakisi, kuti apite ndi gulu lalikulu lankhondo kwa Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo adaima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku malo a mmisiri woyeretsa nsalu.
3Anthu atatu adatuluka mu mzinda nakakumana naye. Anthu ake ndi aŵa: mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu, dzina lake Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika.
4Kazembe wankhondo uja adaŵauza kuti akanene kwa Hezekiya mau aŵa: “Mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya ikuti, ‘Chimene chikulimbitsa chikhulupiriro chako motere nchiyani?
5Kodi ukuganiza kuti mau okha nkulingana ndi luso ndi mphamvu pa nkhondo? Kodi tsono ukudalira yani kuti uzindigalukira?
6Ezek. 29.6, 7 Makamaka ukuyembekeza kuti Ejipito adzakuthandiza. Koma kuteroko kuli ngati kukhulupirira bango lothyoka limene litha kum'baya munthu m'manja ataliyesa ndodo yoyendera. Ndimo m'mene mfumu ya ku Ejipito imamchitira aliyense woidalira.
7“Kapena undiwuza kuti mumakhulupirira Chauta Mulungu wanu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene akachisi ake ndi maguwa ake, Hezekiya adaŵathetsa, nauza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa ili la ku Yerusalemu?”
8Tiye tsono utembezane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ndidzakupatsa akavalo okwanira zikwi ziŵiri ngati iwe ungathe kupeza anthu ake okwerapo.
9Ungathe bwanji kupambana ngakhale mmodzi yekha mwa akazembe ang'onoang'ono a mbuye wanga, pamene ukukhulupirira Aejipito, kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo?
10Ndiponso kodi sukudziŵa kuti ndi Chauta amene wandibweretsa kuno, ndidzathire nkhondo dziko lino ndi kuliwononga? Chautayo ndiye adachita kundiwuza kuti ndilimbane nalo ndi kuliwononga dziko lino.’ ”
11Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda, pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.”
12Koma kazembe uja adati, “Kodi mukuganiza kuti mfumu yanga idandituma kuti ndilankhule mau ameneŵa kwa inu nokha ndi kwa mfumu yanu basi? Iyai, ndikulankhulanso kwa anthu amene akhala pakhomowo, amene adzayenera kudya ndoŵe yao yomwe ndi kumwa mkodzo wao womwe, monga momwe mudzachitire inuyo.”
13Tsono kazembe uja adaimirira nafuula m'Chiyuda kuti, “Mverani mau a mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya.
14Mfumuyo ikuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akunyengeni, chifukwa sadzatha kukupulumutsani.
15Asakukakamizeni kuti mudalire Chauta pokuuzani kuti mosapeneka konse Chauta wanuyo adzakupulumutsani, ndipo kuti mfumu ya ku Asiriya sidzalanda mzinda wanuwu.
16Musamumvere Hezekiya. Mfumu ya ku Asiriya ikukulamulani kuti mutulukemo mumzindamo, ndipo muigonjere. Mukatero, aliyense mwa inu azidzadya mphesa ndi nkhuyu zake ndi kumamwa madzi a m'chitsime chake,
17mpaka nthaŵi imene mfumuyo idzakutengeni kupita nanu ku dziko lolingana ndi lanuli, dziko la mwana alirenji.
18Ndiye inu chenjerani, Hezekiya asakupusitseni pokuuzani kuti Chauta adzakupulumutsani. Mwa milungu ya anthu a mitundu ina, kodi alipo ndi mmodzi yemwe amene adapulumutsapo dziko lake kwa mfumu ya ku Asiriya?
19Kodi milungu ya Hamati ndi Aripadi ili kuti tsopano? Nanga milungu ya Sefaravaimu ili kuti? Kodi milunguyo idaupulumutsa mzinda wa Samariya kwa mbuye wanga?
20Kodi ndi iti mwa milungu ya maikoŵa imene idapulumutsapo maiko ake kwa mfumu yathu, kuti inu muziti Chauta nkupulumutsa Yerusalemu kwa mfumu yathuyo?’ ”
21Koma anthu adangokhala chete osayankhapo kanthu, chifukwa mfumu Hezekiya adaaŵalamula kuti, “Musamuyankhe ai.”
22Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya amene ankayang'anira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika, adang'amba zovala zao mwachisoni, ndipo adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza zimene kazembe wa ku Asiriya uja adaalankhula.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.