Owe. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Samisoni ku Gaza.

1Samisoni adapita ku Gaza ndipo kumeneko adaonako mkazi wadama naloŵa m'nyumba yake.

2Anthu a ku Gaza adauzidwa kuti, “Samisonitu adabwera kuno.” Tsono anthuwo adazinga malowo namubisalira usiku wonse pa chipata cha mzinda. Iwo adakhala chete usiku wonsewo namanena kuti, “Tiyeni tidikire mpaka m'maŵa kutacha, pamenepo timuphe.”

3Koma Samisoni adagona mpaka pakati pa usiku. Pakati pa usikupo adadzuka, nagwira zitseko zapachipata ndi mafuremu ake onse aŵiri. Adazizula pamodzi ndi mpiringidzo ndi zina zonse. Adazisenza pa phewa, napita nazo pamwamba pa phiri loyang'anana ndi Hebroni.

Samisoni ndi Delila.

4Pambuyo pake Samisoni adayamba kukonda mkazi wina wa ku chigwa cha Soreki, dzina lake Delila.

5Akalonga a Afilisti adabwera kwa mkaziyo namuuza kuti, “Umnyengerere mwamunayu, uwone pamene pagona mphamvu zake zoopsazi ndiponso m'mene tingathe kumpambanira, kuti timmange ndi kumgonjetsa. Ukatero, aliyense mwa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.”

6Tsono Delila adauza Samisoni kuti, “Inu, tandiwuzani, kodi mphamvu zanu zoopsazi zagona poti? Kodi munthu atati akumangeni kuti akugonjetseni, nkofunika kuti atani?”

7Samisoni adamuuza kuti, “Atandimanga ndi nsinga zatsopano zisanu ndi ziŵiri zosauma, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”

8Tsono akalonga a Afilisti aja adadzampatsa mkaziyo nsinga zisanu ndi ziŵiri zatsopano zosauma, ndipo iye adamangira mwamuna wake.

9Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo ataika anthu ombisalirawo m'chipinda cham'kati. Kenaka adafuula kwa mwamuna wake kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adangomwetula nsingazo monga m'mene imamwetukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zakezo sichidadziŵikebe.

10Apo Delila adauza Samisoni kuti, “Ndithu mwandipusitsa ndi kundinamiza. Chonde tandiwuzani m'mene munthu angakumangireni.”

11Samisoni adauza mkaziyo kuti, “Atandimanga ndi zingwe zatsopano zimene sadazigwiritse ntchito, ndidzasanduka wofooka, ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”

12Choncho Delila adatenga zingwe zatsopano nammanga nazo, nafuula kwa iye kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Monsemo nkuti anthu amene ankambisalira aja ali m'chipinda cham'kati. Koma, Samisoni adangomwetula zingwezo kumanja kwake ngati thonje.

13Pamenepo Delila adauzanso Samisoni kuti, “Mpaka tsopano lino mwakhala mukundipusitsa ndi kumandinamiza. Tandiwuzani m'mene munthu angathe kukumangirani.” Samisoni adamuuza kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziŵiri za kumutu kwanga uzilukirira m'cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi anthu ena.”

14Choncho pamene Samisoni ankagona, Delila adatenga njombi za kumutu kwa Samisoni nazilukirira m'cholukira nsalu. Ndipo adachimanga molimbika ndi chikhomo nafuula kwa Samisoni kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adadzukira kutulo nazula chikhomocho, ndipo njombi zake zidachoka m'cholukira chija.

15Apo mkaziyo adamufunsa kuti, “Mungathe bwanji kunena kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Mwakhala mukundipusitsa katatu konseka, ndipo simudandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.”

16Tsono pamene adampanikiza ndi mau ake tsiku ndi tsiku ndi kumkakamiza, mtima wa Samisoni udatopa mpaka kufuna kufa.

17Choncho adamuululira mkaziyo maganizo ake onse namuuza kuti, “Pamutu pangapa sipanapite lumo, popeza kuti ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu, kuyambira ndili m'mimba mwa mai wanga. Atangondimeta tsitsi langali, mphamvu zanga zidzandichokera. Ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”

18Pamene Delila adaona kuti waulula maganizo ake onse, adatuma uthenga kukaŵaitana akalonga a Afilisti aja ndipo adaŵauza kuti, “Bweraninso kamodzi kokha, pakuti wandiwululira maganizo ake onse.” Tsono akalonga a Afilisti adafika kwa mkazi uja atatenga ndalama m'manja mwao.

19Mkaziyo adamgonetsa tulo Samisoni pamiyendo pake. Ndipo adaitana munthu kuti amete njombi zisanu ndi ziŵiri za kumutu kwa Samisoni. Pamenepo iyeyo adayamba kufooka ndipo mphamvu zake zidamchokera.

20Kenaka Delila adafuula kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Samisoni adadzuka akuganiza kuti, “Ndituluka monga momwe ndimachitira nthaŵi zonse, ndipo ndidzimasula.” Koma sadadziŵe kuti Chauta wamsiya.

21Pompo Afilisti adamgwira namkoloola maso ake, ndipo adapita naye ku Gaza atammanga ndi maunyolo amkuŵa. Kumeneko ankapera pa mphero m'ndende.

22Pambuyo pake tsitsi la kumutu kwake lomwe adaalimeta, lidayamba kumeranso.

Samisoni amwalira.

23Tsiku lina akalonga a Afilisti adasonkhana kudzapereka nsembe yaikulu kwa Dagoni mulungu wao ndi kudzakondwerera, pakuti ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa Samisoni, mdani wathu.”

24Pamene anthu adamuwona, adayamba kutamanda mulungu wao. Ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa mdani wathu, munthu woononga dziko lathu uja amene adapha anthu ambiri.”

25Pamene mitima yao inkasangalala adati, “Muitaneni Samisoni kuti adzatisangalatse.” Choncho adamtulutsa m'ndende, ndipo iye adayamba kuŵasangalatsa. Kenaka adamuimiritsa pakati pa mizati.

26Apo Samisoni adauza mnyamata amene adamgwira dzanja kuti, “Undilole ndikhudze mizati imene yachirikiza nyumba yonseyi, kuti ndiitsamire.”

27M'menemo nkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu, amuna ndi akazi. Akalonga onse a Afilisti anali momwemo, ndipo padenga pake panali pafupi anthu 3,000, amuna ndi akazi, amene ankaonera Samisoni akuseŵera.

28Tsono Samisoni adatama Chauta mopemba nati, “Inu Chauta, kumbukireni kamodzi kokhaka, ndapota nanu, ndipo mundilimbitse Inu Mulungu, kuti ndiŵalipsire Afilistiŵa chifukwa cha maso anga aŵiriŵa.”

29Pomwepo Samisoni adagwira mizati iŵiri yapakati imene inkachirikiza nyumbayo. Adaitsamira ndi mphamvu zake zonse, dzanja lake lamanja lili pa mzati wina, lamanzere lili pa mzati winanso.

30Ndipo Samisoni adati, “Ndifere kumodzi ndi Afilistiŵa.” Tsono adakankha ndi mphamvu zake zonse, ndipo nyumbayo idaŵagwera akalonga aja pamodzi ndi anthu onse aja amene anali m'menemo. Choncho kuchuluka kwa anthu amene Samisoni adaŵapha pa nthaŵi ya kufa kwake kudaposa kwa anthu amene iye adaŵapha pa nthaŵi imene anali moyo.

31Tsono abale a Samisoni adabwera pamodzi ndi banja lao lonse kudzamtenga ndipo adakamuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m'manda a Manowa bambo wake. Samisoni adatsogolera Aisraele zaka makumi aŵiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help