Yes. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsoka kwa amene amapanga malamulo

opanda chilungamo,

ndi kwa alembi amene amalemba

zongovutitsa anzao.

2Pakutero amapotoza malamulo poweruza

amphaŵi mosalungama.

Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka,

amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!

3Kodi mudzatani pa tsiku lachilango

pofika namondwe wochokera kutali?

Kodi mudzathaŵira kwa yani kuti akuthandizeni?

Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?

4Kudzatsala nkungozyolika mwamanyazi

pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa

pamodzi ndi ophedwa.

Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke

chifukwa cha zonsezi,

ndipo mkono wake uli chisamulirecho

kufuna kuŵalanga.

Mfumu ya ku Asiriya idzakhala ngati chida cha Mulungu

5 Yes. 14.24-27; Nah. 1.1—3.19; Zef. 2.13-15 Chauta akuti,

“Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya,

mkwapulo wa ukali wanga,

ndodo ya mkwiyo wanga.

6Ndikumtuma kwa mtundu wosasamala za Mulungu,

ndipo ndikumlamula kuti apite kwa

anthu amene ndaŵakwiyira,

kuti akafunkhe ndi kukalanda chuma

chao chonse,

ndi kuŵaponderezera pansi ngati

matope am'miseu.”

7Koma mfumu ya ku Asiriya sikudziŵa

zimenezi ndipo mtima wake sukuganiza choncho.

Mtima wake uli pa kuwononga

ndi kupulula mitundu yochuluka ya anthu.

8Iye akuti:

“Kodi atsogoleri anga onse ankhondo

si mafumu okhaokha?

9Ine ndagonjetsa mizinda iyi:

Kalino, Karikemisi, Hamati, Aripadi.

Ndagonjetsanso Samariya ndi Damasiko.

10Ine ndidakantha mafumu a anthu opembedza mafano,

amene mafano ao ndi aakulu kupambana

a ku Yerusalemu ndi a ku Samariya.

11Ndiye ndingalephere kuwononga

Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake omwe,

monga momwe ndidachitira Samariya ndi mafano ake?”

12Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake.

13Pakuti mfumuyo ikuti,

“Ndachita zimenezi ndi mphamvu

zanga ndiponso ndi nzeru zanga,

pakuti kumvetsa nkwanga.

Ndachotsa malire a mitundu ya anthu,

ndipo ndafunkha chuma chao.

Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu.

14Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu,

monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame.

Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa,

ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi.

Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe

yoti mapiko phephere-phephere,

kapena yoti kukamwa yasa

kapena yolira kuti psepsepse.”

15Koma Chauta akuti:

“Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza

kupambana munthu woigwiritsa ntchito?

Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana

munthu woigwiritsa ntchito?

Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo

ukuzunguza munthu,

kapena ndodo yanyamula munthu!”

16Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse,

adzatumiza matenda oondetsa kwa

ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya.

Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa

ndi moto wosazimika.

17Mulungu, Kuŵala kwa Israele,

adzakhala ngati moto.

Mulungu, Woyera Uja wa Israele,

adzakhala ngati malaŵi a moto.

Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza

ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.

18Adzaononga nkhalango yaikulu ndi

nthaka yachonde.

Zidzaonongeka m'kati ndi kunja kwake,

ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuwonda.

19Mitengo yotsalira yam'nkhalangomo

idzakhala yochepa kwambiri,

yoti ndi mwana yemwe nkuiŵerenga.

Oŵerengeka okha adzabwerera

20Tsiku limenelo otsalira a ku Israele, opulumuka a m'banja la Yakobe, sadzadaliranso anthu amene adaŵakantha, koma ndithu adzadalira Chauta, Woyera Uja wa Israele.

21Otsalira adzabwerera, otsalira a m'banja la Yakobe, adzabwereradi kwa Mulungu wamphamvu.

22Aro. 9.27 Iwe Israele, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wakunyanja, otsalira oŵerengeka okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.

23Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzaononga ndithu dziko lonse monga momwe adalamulira.

Kulangidwa kwa Aasiriya

24Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, akunena kuti, “Inu anthu anga okhala ku Ziyoni, musaŵaope Aasiriya pamene akukanthani ndi ndodo, nakumenyani ndi zibonga zao, monga m'mene Aejipito ankachitira.

25Patsala pang'onong'ono kuti uthe mkwiyo wanga pa inu, koma ndidzaŵakwiyira iwonso mpaka kuŵaononga.

26Ine, Chauta Wamphamvuzonse, ndidzaŵakwapula monga momwe ndidakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu. Ndi ndodo yanga ndidzaŵalanga, monga momwe ndidalangira Aejipito panyanja paja.

27Tsiku limenelo ndidzakusanjulani katundu wa Aasiriya pa mapewa anu, ndi goli lao m'khosi mwanu, golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa.”

Kufika kwa adani

28Adani aja akudza

afika ku Aiyati.

Apyola ku Migironi,

aikiza katundu wao ku Mikimasi.

29Adzera pa mpata uja,

nagona ku Geba usiku.

Anthu a ku Rama akunjenjemera,

a ku Gibea, mzinda wa Saulo, athaŵa.

30Lirani mokweza, inu anthu a ku Galimu!

Tcherani khutu, inu anthu a ku Laisa!

Yankhani, inu a ku Anatoti.

31Anthu a ku Madimena akuthaŵa,

a ku Gebimu akubisala.

32Lero lomwe lino adaniwo adzaima ku Nobu,

adzagwedeza mikono yao

kuwopseza anthu a ku phiri la Ziyoni,

phiri la Yerusalemu.

33Koma Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse,

adzaŵadula ngati nthambi za mtengo.

Akuluakulu adzagwetsedwa,

odzikweza adzatsitsidwa.

34Chauta adzaŵadula

monga momwe anthu amadulira ndi nkhwangwa

mitengo ya m'kati mwa nkhalango.

Iwo adzagwa monga momwe imagwera

ngakhale mitengo yaikulu ya ku Lebanoni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help