1“Ndithudi, ndatopa nawo moyo wanga,
choncho ndidzalankhula zodandaula zanga momasuka.
Ndidzaulula zoŵaŵa zonse zamumtima.
2Ndidzauza Mulungu kuti,
Inu Mulungu, musandiweruze kuti ndine wolakwa.
Koma mundidziŵitse
chifukwa chimene mukukanganirana nane.
3Kodi inu zikukukomerani kuti
mundizunze ndi kundinyoza ine, ntchito ya manja anune,
chonsecho mukukondera upo wa anthu oipa?
4Kodi maso anu ali ngati a munthu?
Kodi mumaona zinthu monga m'mene amaziwonera munthu?
5Kodi masiku anu ndi aafupi
monga m'mene aliri masiku a munthu?
Kodi zaka zanu zili ngati zaka za munthu?
6Chifukwa chiyani tsono mukufufuza zolakwa zanga?
Chifukwa chiyani mukufuna kundipeza mlandu?
7 Lun. 16.15 Koma chonsecho mukudziŵa bwino lomwe
kuti ine ndine wosalakwa,
kuti palibe ndi mmodzi yemwe amene
angandipulumutse m'manja mwanu.
8“Mudandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu.
Koma tsopano mukufuna kundiwononga ndi manja anu omwewo.
9Musaiŵale kuti paja mudandipanga ndi dothi.
Kodi mukufuna kundibwezeranso kufumbi komweko?
10 Lun. 7.1, 2 Suja mudapatsa bambo wanga mphamvu zoti andibale,
suja mudandikuza bwino m'mimba mwa mai wanga?
11Mudandikuta ndi khungu ndi mnofu,
mudalumikiza mafupa anga ndi mitsempha.
12Mudandipatsa moyo mwa chikondi chanu chosasinthika,
mudandisamala bwino kuti moyo wanga ulimbike.
13Nthaŵi yonseyo munkabisa zolinga zanu.
Koma tsopano ndikuŵadziŵa maganizo anu.
14Munkapenyetsetsa kuti muwone ngati nditi ndichimwe.
Munali wosafuna kukhululukira tchimo langa lililonse.
15Mukandipeza wolakwa, tsoka langa!
Ngakhale mundipeze wosalakwa, ndigwetsabe nkhope,
pakuti ndagwidwa ndi manyazi, poona mavuto angaŵa.
16Ndikadzilimbitsa mtima,
mumakhala ngati mkango wondisaka,
mumafuna kundiwopsa ndi mphamvu zanu.
17Mumandiikiranso mboni zondineneza,
mkwiyo wanu umanka nukulirakulira.
Magulu anu olimbana nane akunka nachulukirachulukira.
18“Inu Mulungu, chifukwa chiyani mudandibadwitsa ineyo?
Achikhala ndidaangofa, wina aliyense asanandiwone.
19Achikhala ndidaachita ngati mtayo basi,
akadanditenga pobadwapo nkupita nane ku manda.
20Kodi masiku a moyo wanga si oŵerengeka chabe?
Ingondilekani kuti ndipumuleko pang'ono,
21ndisanapite kumene sindidzabwerako,
dziko la imfa, kumene kuli mdima wandiweyani,
22ku dziko lamdimatu ndi lachisokonezo,
kumene ngakhale kuŵala kudasanduka mdima.”
Zofari
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.