Hos. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chilango chotsiriza cha Israele

1Kale Aefuremu ankati akalankhula,

anthu ankachita mantha

chifukwa ankalemekezeka m'dziko la Israele,

koma adalakwa popembedza Baala, motero adzafa.

2Masiku ano akuchimwirachimwira.

Akudzipangira mafano oumba

pogwiritsa ntchito siliva wao.

Mafano onsewo ndi ntchito ya anthu aluso.

Amati, “Perekani nsembe kwa ameneŵa,

pembedzani anaang'ombeŵa poŵampsompsona.”

3Nchifukwa chake adzazimirira ngati nkhungu yam'maŵa,

kapena mame okamuka msanga.

Adzamwazika ngati mungu wouluzika

kuchokera pa malo opunthira tirigu,

kapena ngati utsi wotuluka pa zenera.

4Chauta akuti

“Ine ndakhala Chauta Mulungu wako

kuyambira nthaŵi imene ndidakutulutsa ku Ejipito.

Sudziŵa Mulungu wina, koma Ine ndekha,

Mpulumutsi wako ndine ndekha.

5 Deut. 8.11-17 Ndine ndidakusamalani m'chipululu,

m'dziko lotentha kwambiri.

6Ndidaŵadyetsa, nakhuta,

koma atakhuta, adanyada,

ndipo adandiiŵala Ine.

7Motero ndidzaŵalumphira ngati mkango,

ndidzaŵalalira ngati kambuku m'mbali mwa njira.

8Ndidzaŵambwandira

ngati chimbalangondo cholandidwa ana.

Ndidzathyola nthiti zao,

ndipo ndidzaŵamwamwata pomwepo ngati mkango,

ndidzaŵankhanthula ngati chilombo choopsa.

9“Ndidzaononga inu Aisraele.

Kodi ndani angakuthandizeni?

10 1Sam. 8.5, 6 Inu munkati,

‘Tipatseni mfumu ndi atsogoleri.’

Nanga tsopano mfumu yanuyo,

yoti ikulanditseni,

ili kuti?

Nanga atsogoleri anuwo,

oti akutchinjirizeni,

ali kuti?

11 1Sam. 10.17-24; 1Sam. 15.26 Ndidakupatsani mafumu mwachipsera mtima.

Kenaka atandikwiyitsa, ndidaŵachotsa.

12“Kuipa kwa anthu a ku Efuremu kwalembedwa m'buku,

buku lake la machimo ao ndalisunga.

13Zoŵaŵa zonga za mkazi pobala mwana zidzaŵagwera.

Akadapulumutsidwa,

koma ali ngati mwana wopanda nzeru,

wosafuna kutuluka pa nthaŵi yake yobadwa.

14 1Ako. 15.55 Kodi ngati ndidzaŵapulumutsa kwa akufa?

Kodi ngati ndidzaŵaombola ku imfa?

Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti?

Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti?

Anthu ameneŵa sindidzaŵachitiranso chifundo.

15Ngakhale kuti Efuremu akondwe ngati bango,

mphepo yakuvuma mphepo ya Chauta,

idzakuntha kuchokera kuchipululu.

Motero kasupe wake adzaphwa,

ndipo chitsime chake chidzauma.

Adani adzaononga chuma chake chamtengowapatali.

16A ku Samariya adzalangidwa

chifukwa choti adapandukira Mulungu wao.

Adzaphedwa ndi lupanga,

ana ao adzaphedwa moŵakankhanthitsa pansi.

Akazi ake apathupi adzang'ambidwa.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help