1Inu Chauta, onetsani kuti ine ndine wosalakwa,
pakuti ndimachita zolungama,
ndipo ndakhulupirira Inu mosakayika konse.
2Mundiyang'anitsitse, Inu Chauta, ndi kundiyesa.
Muwone mtima wanga pamodzi ndi maganizo anga.
3Chikondi chanu chimanditsogolera,
ndipo ndimakhala wokhulupirika kwa Inu.
4Sindikhala pamodzi ndi anthu onyenga,
sindiyenda ndi anthu achiphamaso.
5Ndimadana ndi anthu ochita zoipa,
sindikhala pamodzi ndi anthu oipa.
6Ndimasamba m'manja kuwonetsa kuti sindidachimwe,
ndimakupembedzani pa guwa lanu lansembe, Inu Chauta.
7Ndimaimba molimbika nyimbo yothokozera,
ndimalalika ntchito zanu zonse zodabwitsa.
8Inu Chauta, ndimakonda Nyumba imene mumakhalamo,
ndiye kuti malo amene kuli ulemerero wanu.
9Musanditayire kumodzi ndi anthu ochimwa,
musandichotsere moyo
pamodzi ndi anthu ofuna kupha anzao,
10anthu amene manja ao amachita zoipa,
ndipo anthu amene dzanja lao lamanja
ndi lodzaza ndi ziphuphu.
11Koma ine ndimayenda mokhulupirika,
mundikomere mtima ndipo mundipulumutse.
12Ndili wokhazikika pa malo opanda zovuta,
ndipo ndidzatamanda Chauta pa msonkhano waukulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.