Lev. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kasamalidwe ka nyale(Eks. 27.20-21)

1Chauta adauza Mose kuti,

2“Lamula Aisraele kuti akupatse mafuta anyale, a olivi wabwino kwambiri, kuti nyale izikhala yoyaka nthaŵi zonse m'Nyumba mwanga.

3Aroni aiyatse nyaleyo pamaso pa Chauta kunja kwa nsalu yochinga bokosi lachipangano, limene lili m'chihema chamsonkhano, kuti ikhale chiyakire kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse.

4Aroni ayatse nyale zimene zili pa choikapo chake cha golide wabwino kwambiri, kuti zikhale zoyaka nthaŵi zonse pamaso pa Chauta.

Za buledi wopereka kwa Mulungu

5 Eks. 25.30 “Mutenge ufa wosalala, ndipo muphike makeke khumi ndi aŵiri. Keke iliyonse ikhale ya ufa wokwanira makilogaramu aŵiri.

6Muŵaike m'mizere iŵiri pa tebulo la golide wabwino kwambiri, mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi.

7Pa mzere uliwonse muikepo lubani wokoma, kuti pamodzi ndi bulediyo akhale chikumbutso cha nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta.

8Pa tsiku la Sabata lililonse Aroni aziika makeke a nsembeyo mosalephera pamaso pa Chauta m'malo mwa Aisraele, kuti chikhale chipangano chamuyaya.

9Mt. 12.4; Mk. 2.26; Lk. 6.4 Chakudyacho chikhale cha Aroni ndi ana ake, ndipo achidyere m'malo oyera, pakuti kwa iyeyo chimenecho nchopatulika kopambana, chochokera pa nsembe yopsereza kwa Chauta. Lamuloli ndi lamuyaya.”

Za chilango cholungama

10Tsiku lina munthu wina amene mai wake anali Wachiisraele, koma bambo wake anali wa ku Ejipito, adapita kwa Aisraele ndipo adakangana ndi Mwisraele mmodzi ku mahema.

11Munthu uja adanyoza dzina la Chauta ndi kulitemberera. Tsono adabwera naye kwa Mose. Dzina la mai wake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.

12Adamuika m'ndende mpaka atadziŵa kufuna kwa Chauta.

13Chauta adauza Mose kuti,

14“Umtulutse kuzithandoko munthu wotembererayo. Onse amene adamumva akutemberera asanjike manja ao pamutu pake, kutsimikiza kuti ndi wochimwadi, ndipo mpingo wonse umponye miyala.

15Tsono uza Aisraele kuti, ‘Aliyense wotemberera Mulungu wake alangidwe,

16wonyoza dzina la Chauta ayenera kuphedwa. Mpingo wonse umponye miyala. Mlendo kapena mbadwa akangonyoza dzina la Chauta, ayenera kuphedwa.

17Eks. 21.12 Munthu wopha mnzake ayenera kuphedwa.

18Munthu wopha choŵeta cha mnzake amlipire china, moyo ulipe moyo.

19Munthu akapundula mnzake, nayenso amchite zomwezo.

20Eks. 21.23-25; Deut. 19.21; Mt. 5.38 Kuphwanya fupa kulipe kuphwanya fupa, diso lilipe diso, dzino lilipe dzino. Monga momwe munthu adapundulira mnzake, nayenso amchite zomwezo.

21Munthu wopha choŵeta cha mnzake, alipire china, koma munthu wopha mnzake ayenera kuphedwa.

22Num. 15.16 Lamulo la mlendo ndi mbadwa likhale limodzi lomwelo. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ”

23Mose adauza Aisraele zimenezi, ndipo iwo adatulutsa munthu wotemberera uja m'zithandomo, namponya miyala. Motero Aisraele adachita zimene Chauta adalamula Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help