Yes. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mtendere wamuyaya

1Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya, mwana wa Amozi, adaziwona m'masomphenya.

2Pa masiku akudzaŵa

phiri la Nyumba ya Chauta

adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse,

lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse.

Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo.

3Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti,

“Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta,

ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe.

Iye adzatiphunzitsa njira zake,

ndipo tidzayenda m'njira zakezo.”

Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo,

nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.

4 Yow. 3.10; Mik. 4.3 Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu,

adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri.

Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu,

ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika.

Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga,

sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.

5Inu zidzukulu za Yakobe,

tiyeni tiyende m'kuŵala kwa Chauta.

Tsiku la Chauta

6Inu Mulungu, mwakana anthu anu,

zidzukulu za Yakobe.

Dziko ladzaza ndi anthu amatsenga akuvuma,

ladzazanso ndi olosa a ku Filistiya.

Anthu anu akuchita nao miyambo yachilendo.

7Dziko la anthu anu nlodzaza ndi siliva ndi golide,

ndipo chuma chao nchosatha.

Dziko lao nlodzaza ndi akavalo,

ndipo magaleta ao ankhondo ndi osaŵerengeka.

8Dziko lao nlodzaza ndi mafano.

Iwo amapembedza mafano opanga ndi manja ao,

oumba ndi zala zao zomwe.

9Nchifukwa chake adzaŵachepetsa ndi kuŵatsitsa.

Inu Chauta, musaŵakhululukire!

10 Chiv. 6.15; 2Ate. 1.9 Loŵani m'matanthwe,

bisalani m'maenje kuti muthaŵe mkwiyo wa Chauta,

muthaŵenso ulemerero wa ufumu wake.

11Kudzikuza kwa anthu kudzatha,

kudzitama kwa anthu kudzaonongedwa.

Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.

12Chauta Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku,

pamene adzatsitsa onse onyada ndi odzitama,

ndipo adzagonjetsa onse amphamvu.

13Adzadula mikungudza yonse ya ku Lebanoni,

italiitali kopambana ina yonse.

Adzalikha mitengo yonse ya thundu ya ku Basani.

14Adzasalaza mapiri onse aatali.

Adzafafaniza magomo onse okwera.

15Adzagwetsa nsanja zonse zazitali.

Adzagumula malinga onse olimba.

16Adzamiza zombo zonse za ku Tarisisi.

Adzaononga mabwato onse okongola.

17Kudzikuza kwa anthu kudzatha,

kudzitama kwao konse kudzaonongedwa.

Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.

18Mafano onse adzatheratu.

19Anthu adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe

ndi m'maenje am'nthaka,

kuthaŵa mkwiyo wa Chauta,

kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake,

pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.

20Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme

mafano asiliva ndi agolide,

amene adaadzipangira kuti azipembedza.

21Adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe

ndi m'ming'alu yam'nthaka,

kuthaŵa mkwiyo wa Chauta,

kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake,

pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.

22Musakhulupirirenso munthu,

poti moyo wake sukhalira kutha.

Nanga iye nkumuyesanso kanthu ngati!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help