Ezek. 47 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kasupe wotuluka m'Nyumba ya Mulungu

1 Zek. 14.8; Yoh. 7.38; Chiv. 22.1 Tsono munthu uja adabwerera nane ku chipata cha ku Nyumba ya Mulungu. Ndidaona kasupe akutuluka kunsi kwa chiwundo choloŵera ku Nyumba ya Mulungu chakuvuma, poti Nyumbayo inali yoyang'ana kuvuma. Kunkayenda madzi kunsi kwa chipupa chakumwera cha Nyumba ya Mulungu, chakumwera kwa guwa.

2Adanditulutsira pa chipata chakumpoto, nazungulira nane panja pake mpaka ku chipata chakunja choyang'ana kuvuma. Ndipo ndidaona madzi akutuluka chakumwera kwa chipata.

3Munthuyo adapita chakuvuma ali ndi choyesera m'manja mwake, nayesa mamita mazana asanu. Kenaka adandiwuza kuti ndiloŵe m'madzimo. Madziwo adandilekeza m'kakolo.

4Adayesanso mamita mazana asanu, nandiloŵetsanso m'madzi muja, ndipo madziwo adandilekeza m'chiwuno.

5Adayesanso mamita mazana asanu, ndipo madzi adasanduka mtsinje ndithu, ine osatha kuwoloka, poti madziwo adaakwera, anali ozama kwambiri olira kusambira poŵaoloka.

6Apo adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, waziwonatu zimenezi ati?” Atatero adandibwezera ku gombe la mtsinjewo.

7Titafika kugombeko, ndidaona mitengo yambiri pa mbali iliyonse ya gombelo.

8Tsono munthuyo adandiwuza kuti, “Madzi ameneŵa akupita ku chigawo chakuvuma cha dziko kutsikira ku chigwa cha Araba. Potsiriza pake, akakathira m'Nyanja Yakufa imene madzi ake ali oipa, madziwo adzakoma.

9Kumene mtsinjewo ukuyenda, cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo, nsombanso zidzachuluka. Pakuti madzi ameneŵa amapita kumeneko kuti akometse madzi anzake. Ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda, zonse zidzakhala ndi moyo.

10Asodzi a nsomba adzakhala pa madooko ao, chifukwa kuyambira ku Engedi mpaka ku Enegilaimu kudzakhala malo abwino oponyako akombe. Mumtsinjewo mudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga za m'Nyanja Yaikulu.

11Koma mataŵale ake ndi maiŵe ake sadzakhala ndi madzi abwino, adzakhalabe amchere.

12Chiv. 22.2Pambali pa mtsinjewo, pa gombe lililonse, padzakhala mitengo yobereka zipatso za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota, ndipo zipatso zake zidzakhala zosalekeza. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake ndi ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya, ndipo masamba ake azidzachita mankhwala.”

Malire a dziko

13Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Naŵa malire amene mudzatsate poŵagaŵira dziko la Israele mafuko khumi ndi aŵiri aja: Yosefe alandire zigawo ziŵiri.

14Dzikoli mudzagaŵana mofanana, chifukwa ndidalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu ndipo lidzakhala lanulanu. Motero lidzapatsidwa kwa inu mwamaere, kuti likhale choloŵa chanu.

15Malire ake adzayende motere: chakumpoto kwake achokere ku Nyanja Yaikulu, kutsata mseu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kupitirira ku Zedati,

16Berata ndi Sibraimu, mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati, mpaka ku Hazere-Hatikoni pafupi ndi malire a Haurani.

17Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazarenoni umene wachitana malire ndi Damasiko chakumpoto, ndiponso mpaka m'malire a Hamati chakumpoto. Imeneyi ndiyo idzakhala mbali yakumpoto.”

18“Malire akuvuma ayende chakumwera kuchokera ku Hazarenoni pakati pa Haurani ndi Damasiko, kutsata mtsinje wa Yordani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israele, kuloza ku nyanja yakuvuma mpaka ku Tamara. Imeneyi idzakhala mbali yakuvuma.”

19“Malire akumwera ayende kuchokera ku Tamara mpaka ku dziŵe la Meriboti-Kadesi. Kuchokera kumeneko atsate malire a ku Ejipito mpaka ku Nyanja Yaikulu. Imeneyi ndiyo mbali yakumwera.”

20“Malire akuzambwe akhale Nyanja Yaikulu mpaka ku malo oyang'anana ndi chipata cha Hamati. Imeneyi ndiyo mbali yakuzambwe.”

21“Motero mugaŵane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israele.

22Muligaŵe kuti likhale choloŵa chanu. Likhalenso la alendo amene amakhala pakati panu, nabereka ana pakati panu. Alendowo adzakhala nanu ngati mbadwa za mu Israele. Adzapatsidwa choloŵa chao pamodzi ndi inuyo.

23Mlendo aliyense umpatse choloŵa chake ku fuko limene akukhalakolo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help