2 Sam. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aminoni ndi mlongo wake Tamara.

1Abisalomu mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola, dzina lake Tamara. Aminoni, mwana wina wa Davide, ankakonda Tamara.

2Iye sankagona tulo chifukwa cha Tamara mlongo wake, mpaka kuchita kudwala. Tamarayo anali namwali wosadziŵa mwamuna, ndipo kunkaoneka kuti chinali chosatheka kuti Aminoniyo amchite chilichonse.

3Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wake wa Davide. Yonadabuyo anali munthu wochenjera kwambiri.

4Tsiku lina Yonadabu adafunsa Aminoni kuti, “Kodi iwe, mwana wa mfumu, chifukwa chiyani umaoneka woonda m'maŵa masiku onse? Bwanji osandiwuza ine?” Aminoni adamuyankha kuti, “Ine ndikukonda Tamara, mlongo wa mkulu wanga Abisalomu.”

5Tsono Yonadabu adamuuza kuti, “Kagone pabedi pako, ndipo uchite ngati wadwala. Bambo wako akafika kuti adzakuwone, umuuze kuti, ‘Mloleni Tamara, mlongo wanga, abwere andikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho konkuno, ine ndikupenya, kuti ndichiwone, ndipo ndidzadyere m'manja mwake.’ ”

6Choncho Aminoni adagona, nachita ngati wadwala. Mfumu itabwera kudzamuwona, Aminoniyo adauza mfumuyo kuti, “Chonde, mulole mlongo wanga Tamara abwere, kuti adzandiphikire chakudya ine ndikupenya, kuti ndidzadyere m'manja mwake.”

7Davide adatumiza mau kwa Tamara kuti, “Upite kunyumba kwa mbale wako Aminoni, ukamphikire chakudya.”

8Tamara adapitadi kunyumba kwa mbale wake Aminoni ku malo kumene ankagona. Adatenga ufa, naukanda, naumba makeke, Aminoniyo akupenya, ndipo adaphika makekewo.

9Tsono adatenga chiwaya, nakhuthula makekewo, iye akupenya, koma Aminoniyo adakana kudya. Ndipo Aminoni adati, “Uzani anthu onse achoke.” Choncho anthu onse adachoka.

10Tsono Aminoni adauza Tamara kuti, “Bwera nacho chakudya chija m'chipinda muno kuti ndidzadyere m'manja mwako.” Tamara adatenga makeke amene adaaphikawo, napita nawo kwa Aminoni, mbale wake, m'chipindamo.

11Koma atafika nacho chakudyacho pafupi ndi Aminoni kuti adye, Aminoni adamgwira Tamara, namuuza kuti, “Bwera ugone nane, iwe Tamara.”

12Koma Tamarayo adayankha kuti, “Iyai, mlongo wanga, usandikakamize. Zimenezi sizidachitikepo nkale lonse ku Israele. Usachite zauchitsiru zotere.

13Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.”

14Koma Aminoni sadamve zimene ankanena Tamarazo. Ndipo popeza kuti anali ndi mphamvu zoposa Tamara, Aminoniyo adamkakamiza Tamarayo nagona naye.

15Pambuyo pake Aminoni adayamba kudana naye kwabasi Tamarayo, kotero kuti chidani chake ndi Tamara chidakula kwambiri kuposa chikondi chimene adaamkonda nacho. Ndipo Aminoniyo adauza Tamara kuti, “Dzuka, kazipita.”

16Koma Tamarayo adati, “Iyai, mlongo wanga, kundipirikitsa chotere nkulakwa koposa zimene wandichitazi.” Koma Aminoni sadafune kumva zimene ankanena Tamarazo.

17Pomwepo Aminoniyo adaitana mnyamata amene ankamtumikira, namuuza kuti, “Mtulutse mkaziyu, achoke pano, ndisamuwonenso, ndipo upiringidze chitseko iyeyo akatuluka.”

18Nthaŵi imeneyo Tamara adaavala deresi lalitali, la manja aatali, monga momwe ankavalira ana achinamwali a mfumu, amene sadadziŵeko amuna. Tsono mnyamata wa Aminoni uja adatulutsa Tamara, napiringidza chitseko mkaziyo atatuluka.

19Ndipo Tamara adadzithira phulusa kumutu, nang'amba chovala chake chachitali chimene adaavala. Ndipo adagwirira manja kumutu, namapita akulira mokweza njira yonse.

20Apo Abisalomu, mlongo wa Tamarayo, adamufunsa kuti, “Monga Aminoni uja wakuchimwitsa? Komabe, iwe khala phee, mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako. Zimenezi usavutike nazo.” Choncho Tamara ankakhala ngati wofedwa kunyumba kwa mlongo wake Abisalomu.

21Davide atazimva zimenezi, adapsa nazo mtima zedi.

22Koma Abisalomu sadanenepo kanthu kalikonse kabwino kapena koipa kwa Aminoni. Pakuti Abisalomuyo adaamuzonda kwambiri Aminoni chifukwa choti adaakakamiza Tamara mlongo wake kuchita naye zoipa.

Abisalomu apha Aminoni, nkuthaŵa.

23Patapita zaka ziŵiri zathunthu, Abisalomu anali ndi anthu ake ku ntchito yometa nkhosa ku Baala-Hazori pafupi ndi Efuremu. Tsono adaitana ana aamuna onse a mfumu kuti akakhaleko.

24Adapita kwa mfumu nati, “Amfumu, ine mtumiki wanu ndikukachita ntchito yometa nkhosa ndi anthu anga. Ndimati ngati nkotheka mudzakhale nafe inuyo amfumu pamodzi ndi atumiki anu.”

25Koma mfumu idauza Abisalomu kuti, “Iyai, mwana wanga, tisachite kupita tonse, tingakakuvutitse.” Adayesera muno ndi muno kumuumiriza, komabe Davide sadapite nao, m'malo mwake adangomdalitsa Abisalomuyo.

26Tsono Abisalomu adati, “Chabwino, ngati inu simupita, bwanji apite nao ndi mbale wanga Aminoniyu.” Apo mfumu idafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukufuna kuti iyeyu apite nao?”

27Koma Abisalomu adamkakamiza ndithu mpaka Davide adalola kuti Aminoni pamodzi ndi ana onse aamuna a mfumu apite nao.

28Tsono Abisalomu adalamula antchito ake kuti, “Muwonetsetse nthaŵi imene Aminoni akhale ataledzera ndi vinyo. Ndikakuuzani kuti, ‘Kanthani Aminoni!’ Pomwepo mumuphe. Musaope, nanga sindine ndakulamulani? Mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna.”

29Choncho atumiki a Abisalomu adamchita Aminoni monga momwe adaaŵalamulira Abisalomu. Zitatero, ana onse aamuna a mfumu adadzambatuka, aliyense adakwera pa bulu wake, nathaŵa.

30Koma anthuwo akali m'njira, Davide adamva mphekesera zakuti Abisalomu wapha ana onse aamuna a mfumu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsalako.

31Pompo mfumu idadzuka, ning'amba zovala zake, nkudzigwetsa pansi. Atumiki ake onse amene anali pafupi naye, nawonso adang'amba zovala zao.

32Koma Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide, adati, “Mbuyanga, musaganize kuti ana onse a inu mfumu aphedwa, Aminoni yekha ndiye waphedwa. Zimenezi zachitika poti nzimene Abisalomu adaatsimikiziratu kale, kuyambira pa tsiku limene Aminoni adakakamiza Tamara, mlongo wa Abisalomu, kuchita naye zoipa.

33Nchifukwa chake tsono mbuyanga mfumu, musavutike ndi maganizo oti ana anu onse aamuna aphedwa. Aminoni yekha ndiye waphedwa.”

34Nthaŵi imeneyo nkuti Abisalomu atathaŵa. Tsono mlonda wapalinga poyang'ana, adangoona anthu ambiri akuchokera ku mseu wa Horonaimu, m'mbali mwa phiri.

35Atamva zimenezi Yonadabu adauza mfumu kuti, “Ana a mfumu abwera. Amfumu, monga momwe ndinakuuzirani muja, ndi m'mene zayendera.”

36Tsono atangomaliza kulankhula, adangoona ana a mfumu akubwera, ndipo anawo adayamba kubuma maliro. Pomwepo mfumuyo nayonso idalira kwambiri pamodzi ndi atumiki ake.

37 2Sam. 3.3 Abisalomu adathaŵa ndithu napita kwa Talimai, mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide adalira maliro a mwana wake Aminoni nthaŵi yaitali.

38Abisalomu adakhala ku Gesuri zaka zitatu.

39Tsono mfumu Davide adagwidwa ndi chifundo chofuna kumlondola Abisalomuyo. Pamenepo nkuti Davideyo atatonthozedwa pa imfa ya Aminoni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help