Yos. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Dziko la Manase wakuzambwe.

1Gawo lina la dzikolo lidapatsidwa kwa fuko la Manase amene anali mwana wachisamba wa Yosefe. Makiri, kholo la anthu okhala ku Giliyadi, ndiye anali mwana wachisamba wa Manase. Makiri analinso msilikali, motero maiko aŵa, Giliyadi ndi Basani, adapatsidwa kwa iyeyo.

2Mabanja otsala a Manase amene adapatsidwanso dziko ndi aŵa: Abiyezere, Heleki, Asiriele, Sekemu, Hefere ndi Semida. Ameneŵa ndiwo zidzululu za Manase, mwana wa Yosefe, komanso ndiwo amene anali eni mbumba.

3Panali Zelofehadi mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase. Zelofehadiyo analibe mwana wamwamuna ndi mmodzi yemwe, koma aakazi okhaokha. Maina a ana aakaziwo ndi aŵa: Mahala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.

4Num. 27.1-7 Iwoŵa adabwera kwa Eleazara wansembe, nafikanso kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri, ndipo adati, “Chauta adalamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse gawo lina la dziko ngati choloŵa chathu.” Motero iwowo, pamodzi ndi abale a bambo wao, adapatsidwa dziko kuti likhale lao potsata zimene Chauta adalamula.

5Choncho kuwonjeza pa maiko a Giliyadi ndi Basani a kuvuma kwa Yordani, a fuko la Manase adalandiranso magawo khumi,

6popeza kuti ana aakazi a Manase ndi ana ake aamuna, onsewo adalandira magawo ao. Dziko la Giliyadi lidapatsidwa kwa otsala mwa zidzukulu za Manase.

7Dziko la Manase malire ake adachokera ku Asere, ndipo adakafika ku Mikimetati kuvuma kwa Sekemu. Tsono malire adapita kumwera kuloza kwa anthu a ku Entapuwa.

8Dzikolo linali la Manase, koma mzinda wa Tapuwa wapamalire unali wa fuko la Efuremu, ngakhale kuti m'pakati penipeni pa mizinda ya Manase.

9Tsono malire ake adatsikira ku kamtsinje ka Kana. Mizinda yakumwera kwa kamtsinje kameneka inali ya fuko la Efuremu, ngakhale inali m'dziko la Manase. Malire a dziko la Manase adalambalala chakumpoto kwa kamtsinjeko, nakalekezera ku nyanja.

10Efuremu anali kumwera, Manase anali kumpoto, ndipo Nyanja Yaikulu inali malire akuzambwe. Malirewo adakafika ku Asere kumpoto chakuzambwe ndi ku Isakara kumpoto chakuvuma.

11M'dziko la Isakara ndi la Asere munalinso gawo lina la Manase lotchedwa Beteseani, kuphatikizapo midzi yozungulira. Panalinso Akanani amene ankakhala ku Ibleamu, ku Dori mzinda wa m'mbali mwa nyanja, ku Endori, ku Taana ndi ku Megido, pamodzi ndi midzi yake yozungulira.

12Owe. 1.27, 28 Komabe anthu a fuko la Manase sadathe kuŵapirikitsa Akanani okhala m'mizinda imeneyo. Motero Akananiwo adangokhalabe komweko.

13Ngakhale pamene Aisraele anali amphamvu m'dzikomo, sadapirikitse Akanani onse, koma adangoŵasandutsa anthu ogwira ntchito yathangata.

Efuremu ndi Manase wakuzambwe apempha kuti aŵaonjezere dziko.

14Zidzukulu za Yosefe zidafunsa Yoswa kuti, “Bwanji ife mwangotigaŵira gawo limodzi lokha la dziko, kuti likhale choloŵa chathu? Ifetu tilipo ambiri chifukwa Chauta adatidalitsa.”

15Yoswa adaŵayankha kuti, “Ngati mulipo ambiri, ndipo ngati dziko lamapiri la Efuremulo likucheperani, loŵani ku nkhalango, mudule mitengo ndi kudzikonzera malo oti mukhalepo m'dziko la Aperizi ndi Arefaimu.”

16Pamenepo zidzukulu za Yosefezo zidati, “Zoonadi dziko lamapirilo silingatikwanire ife, komanso Akanani amene ali ku zigwa ali ndi magaleta achitsulo, ngakhale amene ali ku Beteseani ndi ponse pozungulira, ndiponso amene ali m'chigwa cha Yezireele.”

17Yoswa adauza zidzukulu za Yosefe za m'fuko la Efuremu ndi la Manase kuti, “Inu mulipo ambiri zedi ndipo ndinu amphamvu. Mudzalandira magawo enanso.

18Mudzalandiradi dziko lamapirilo. Ngakhale lili ndi nkhalango, inuyo mudzadula mitengo, ndipo mudzalandira dziko lonselo kuti likhale lanu. Akanani mudzaŵapirikitsa, ngakhale ali ndi magaleta achitsulo ndiponso ngakhale iwo ngamphamvu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help