1Tsono Rehobowamu adapita ku Sekemu. Apo nkuti Aisraele onse atapita kale ku Sekemuko, kuti akamulonge ufumu.
2Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, ali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, adachokako ku Ejipito.
3Anthu adakamuitana. Choncho Yerobowamu pamodzi ndi Aisraele onse, adadza kwa Rehobowamu namuuza kuti,
4“Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipeputsireko goli lolemetsalo ndi ntchito zoŵaŵa zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.”
5Rehobowamu adaŵauza kuti, “Mukabwerenso kuno patapita masiku atatu.” Choncho anthuwo adachoka.
6Tsono mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Inu mungandilangize zotani kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?”
7Madodawo adamuuza kuti, “Mukaŵachitira chifundo anthu ameneŵa ndi kumaŵasangalatsa, mukalankhula nawo mau abwino, iwowo adzakutumikirani mpaka muyaya.”
8Koma Rehobowamu adanyozera zimene madoda aja adaamlangiza nakapempha nzeru kwa achinyamata anzake amene adaakula naye pamodzi namamtumikira.
9Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti tiŵayankhe anthu ameneŵa amene andipempha kuti, ‘Tipeputsireniko goli limene bambo wanu adatisenzetsa?’ ”
10Achinyamata anzakewo adamuuza kuti, “Anthuwo akupemphani kuti, ‘Bambo wanu adatisenzetsa goli lolemera, koma inu mutipeputsireko.’ Inu tsono mukaŵauze kuti, ‘Chala changa chakaninse nchachikulu kupambana chiwuno cha bambo wanga!
11Ndiye kuti bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, kuyambira pano ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.’ ”
12Tsono Yerobowamu ndi anthu onse adabwera kwa Rehobowamu mkucha wake, monga momwe mfumu idaanenera kuti, “Mubwerenso kuno mkucha.”
13Ndiye mfumuyo idaŵayankha mwankhanza. Idanyonzera malangizo a madoda aja,
14nilankhula potsata malangizo a anyamata anzake, nkunena kuti, “Bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, koma ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.”
15Choncho mfumuyo sidamvere pempho la anthuwo, pakuti Mulungu anali atazikonzeratu zinthuzo kuti zichitikedi zimene Chauta adaalankhula ndi Yerobowamu, mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
16 2Sam. 20.1 Tsono Aisraele onsewo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha kuti,
“Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide?
Sitingayembekeze choloŵa chilichonse m'banja la mwana wa Yese.
Ndiye inu Aisraele, bwererani kumahema kwanu.
Tsopano iwe mwana wa Davide,
udziwonere wekha pa banja lako.”
Choncho Aisraele onsewo adachoka napita ku nyumba zao.
17Koma Rehobowamu adakhala akulamulirabe Aisraele enawo okhala m'mizinda ya ku Yuda.
18Tsono mfumu Rehobowamu adatuma Adoramu amene ankayang'anira ntchito yathangata, koma anthu a ku Israele adamponya miyala mpaka kumupha. Pamenepo, mfumu Rehobowamu adakwera msangamsanga pa galeta lake nathaŵira ku Yerusalemu.
19Motero Aisraele akumpoto adakhala akupandukira banja la Davide mpaka lero lino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.