2 Mbi. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ufumu wa Yehosafati

1Yehosafati, mwana wa Asa, adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake, ndipo adadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Aisraele.

2Adaika magulu ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, ndipo adamanga maboma ankhondo ku dziko la Yuda ndi ku mizinda ya ku Efuremu, imene Asa bambo wake adailanda.

3Chauta anali naye Yehosafati, chifukwa chakuti ankatsata makhalidwe oyambayamba aja a Asa bambo wake. Sadatsate Abaala,

4koma ankatsata Mulungu wa atate ake, ndipo ankasunga malamulo ake, osatsata makhalidwe a Aisraele.

5Nchifukwa chake Chauta adaukhazikitsa ufumuwo m'manja mwake. Anthu onse a ku Yuda ankakhoma msonkho kwa iyeyo. Choncho anali nacho chuma chambiri ndiponso ulemu.

6Iyeyo adalimba mtima pa zinthu za Chauta. Kuwonjezera pamenepo, adathetsa akachisi ndiponso mafano a Aserimu ku Yuda.

7Pa chaka chachitatu cha ufumu wake, Yehosafati adatuma nduna zake, Benihali, Obadiya, Zekariya, Netanele ndi Mikaya, kuti akaphunzitse ku mizinda ya ku Yuda.

8Adapita ndi Alevi aŵa: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asahele, Semiramoti, Yohonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobadoniya. Alevi ameneŵa anali pamodzi ndi ansembe aŵa: Elisama ndi Yehoramu.

9Ankaphunzitsa ku Yuda, ali ndi buku la malamulo a Chauta. Ndipo adayendera mizinda yonse ya ku Yuda, namaphunzitsa pakati pa anthu.

Mphamvu za Yehosafati

10Maufumu onse a m'maiko ozungulira Yuda ankaopa Chauta, ndipo sadachitenso nkhondo ndi Yehosafati.

11Afilisti ena adabwera ndi mphatso kwa Yehosafatiyo, pamodzi ndi siliva wa msonkho. Arabu nawonso adabwera ndi nkhosa zamphongo 7,700 ndi atonde 7,700.

12Ndipo mphamvu za Yehosafati zidanka zikulirakulira. Ku Yuda adamanga malinga ndi mizinda yosungirako zinthu.

13Choncho anali ndi nyumba zikuluzikulu zosungiramo zinthu ku mizinda ya ku Yuda. Ku Yerusalemu anali ndi ankhondo, anthu amphamvu ndi olimba mtima.

14Chiŵerengero chao potsata mabanja ao chinali chotere: Ku Yuda, atsogoleri a zikwi anali aŵa: Adina amene anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 300,000.

15Yehohanani, mtsogoleri wotsatana ndi iyeyo, anali ndi anthu 280,000.

16Amasiya mwana wa Zikiri, mtsogoleri wotsatana naye, amene adaadzipereka mwaufulu ku ntchito ya Chauta, anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 200,000. (Amasiya adadzipereka kutumikira Ambuye.)

17Ku Benjamini, Eliyada munthu wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amauta ndi azishango.

18Yehozabadi anali mtsogoleri wotsatana ndi iyeyo, ndipo anali ndi anthu okonzekera nkhondo 180,000.

19Ameneŵa ndiwo ankatumikira mfumu, pamodzi ndi ena amene mfumu idaŵaika ku mizinda yamalinga ku dziko lonse la Yuda.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help