Fil. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndine, Paulo, amene ndili m'ndende chifukwa cha Khristu Yesu. Ndili limodzi ndi Timoteo, mbale wathu. Tikulembera iwe Filemoni, bwenzi lathu ndi mnzathu wantchito.

2Akol. 4.17Kalata yomweyinso tikulembera Afiya, mlongo wathu, ndi Arkipo, msilikali mnzathu pa nkhondo ya Mulungu, ndiponso mpingo wonse umene umasonkhana kunyumba kwanu.

3Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.

Za chikondi cha Filemoni ndi chikhulupiriro chake

4Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukira m'mapemphero anga.

5Pakuti ndikumva kuti umakonda ndi kukhulupirira Ambuye Yesu, ndi oyera onse a Mulungu.

6Ndimapemphera kuti chikhulupiriro chimene ukugaŵana nawo chigwire ntchito mwamphamvu, kuti udziŵitsitse zabwino zonse zimene timalandira chifukwa cha Khristu.

7Mbale wanga, chikondi chako chandikondweretsa kwambiri ndi kundithuzitsa mtima, pakuti watsitsimutsa mitima ya oyera onse a Mulungu.

Paulo ampempherako chifundo Onesimo

8Tsono, inde nkotheka kuti ndichite kukulamula m'dzina la Khristu zimene uyenera kuchita.

9Komabe chifukwa cha chikondi makamaka ndingochita kukupempha, ine Paulo amene ndili nkhalamba, amenenso ndili m'ndende tsopano chifukwa cha Khristu Yesu.

10Akol. 4.9Ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga mwa Khristu, amene ndidachita ngati kumubala m'ndende muno. Iyeyu ndi Onesimo.

11Kale unalibe naye ntchito, koma tsopano angathe kutithandiza kwambiri tonsefe, iweyo ndi ine ndemwe.

12Ndikumtumizanso kwa iwe tsopano, ndipo pakutero ndikuchita ngati kukutumizira mtima wanga womwe.

13Ndikadakonda kuti akhalebe ndi ine kuno, kuti azinditumikira m'malo mwako, pokhala ndili m'ndende chifukwa cha Uthenga Wabwino.

14Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, kuwopa kuti ungandichitire chinthu chabwinochi mokakamizidwa, osati mwaufulu.

15Kapena Onesimo adangokusiya kanthaŵi pang'ono, kuti udzakhale naye nthaŵi zonse,

16osatinso ngati kapolo, koma kwenikweni ngati mbale wokondedwa. Ine ndimamkonda kwambiri, ndipo iweyo uyenera kumkonda koposa, popeza kuti ndi munthu mnzako ndiponso mkhristu mnzako.

17Tsono ngati umati ndine bwenzi lako, umlandire iyeyu monga momwe ukadandilandirira ineyo.

18Ngati adakulakwirapo, kapena ali ndi ngongole kwa iwe, ngongoleyo ikhale yanga.

19Pano mau aŵa ndikulemba ndi dzanja langalanga kuti, “Ine Paulo ndidzalipira.” Nkosasoŵekera kukukumbutsa kuti paja iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wako womwe wachikhristuwu!

20Tsono, mbale wanga, inenso undithandizeko chifukwa cha Ambuye. Undisangulutseko ngati mbale mwa Khristu.

21Ndikukulembera zimenezi, popeza kuti ndikukhulupirira kuti udzachitadi zimene ndakupempha. Ndikudziŵa kuti udzachita kopitiriranso zimene ndapemphazi.

22Kanthu kenanso ndi aka: undikonzere malo, chifukwa ndikhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero a inu nonse, ndi kundibwezera kwa inu.

Mau otsiriza

23 Akol. 1.7; 4.12 Akukupatsa moni Epafra, amene ali m'ndende pamodzi nane chifukwa cha Khristu Yesu.

24Ntc. 12.12, 25; 13.13; 15.37-39; Akol. 4.10; Ntc. 19.29; 27.2; Akol. 4.10; Akol. 4.14; 2Tim. 4.10; Akol. 4.14; 2Tim. 4.11Akutinso moni anzanga antchito, Marko, Aristariko, Dema, ndi Luka.

25Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima nonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help