1Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya ku Israele, Amaziya mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
2Iyeyo anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yehowadani wa ku Yerusalemu.
3Tsono Amaziya adachita zolungama pamaso pa Chauta, komabe osati nthaŵi zonse monga Davide kholo lake. Ankachita zonse monga m'mene ankachitira Yowasi bambo wake.
4Koma akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu adapitirirabe kupereka nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo.
5Atangolandira mphamvu zonse zaufumu m'manja mwake, Amaziya adapha anyamata ake amene adaapha mfumu ija, bambo wake. Koma ana a anthuwo sadaŵaphe,
6 mwana wake, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake. Azariyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu.
22Azariya adagonjetsa mzinda wa Elati naumanganso nkuubwezera ku dziko la Yuda, bambo wake atamwalira.
Mfumu Yerobowamu wachiŵiri wa ku Israele23Chaka cha 15 cha ufumu wa Amaziya, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adaloŵa ufumu ku Samariya, ndipo adalamulira zaka 42.
24Iyeyo ankachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita kholo lake lija Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
25Yon. 1.1 Adalandanso madera ena amene kale anali a dziko la Israele, kuyambira ku chipata cha Hamati kumpoto mpaka kumwera kukafika ku Nyanja ya Araba. Motero zidachitikadi zimene Chauta, Mulungu wa Israele, adaalankhula kudzera mwa Yona mtumiki wake, mwana wa Amitai, mneneri wa ku Gatihefere.
26Chauta adaona kuti mavuto a Aisraele anali oopsa. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotsala, kapolo kapena mfulu, woti angaŵathandize Aisraelewo.
27Koma Chauta sadaanena kuti adzafafaniza ufumu wa Israele pa dziko lapansi ai. Motero adaŵapulumutsa Aisraele kudzera mwa Yerobowamu mwana wa Yehowasi.
28Tsono ntchito zina zonse za Yerobowamu, makamaka za mphamvu zake, za m'mene ankamenyera nkhondo, ndiponso za m'mene adagonjetsera mzinda wa Damasiko ndi wa Hamati naibwezeranso mizindayo ku Israele, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
29Ndipo Yerobowamu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mafumu a ku Israele. Tsono Zekariya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.