Num. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mafuko a Alevi ndi a Akohati

1Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,

2Mwa ana a Levi muŵerenge ana a Kohati, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

3Muŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira pa ntchito ya m'chihema chamsonkhano.

4Ntchito imene ana a Kohati ayenera kugwira m'chihema chamsonkhanomo ndi iyi: azisamala zinthu zopatulika kopambana.

5Pamene anthu akusamuka pamodzi ndi mahema ao, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe m'chihema chamsonkhano, amasule nsalu yochinga, ndipo aphimbire Bokosi laumboni.

6Pambuyo pake ayalepo zikopa zambuzi, ndipo pamwamba pake ayalepo nsalu yobiriŵira, ndi kupisa mphiko m'zigwinjiri zake.

7Ayale nsalu yobiriŵira pa tebulo la buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse, ndi kuikapo mbale zake, zipande zake zotapira lubani, mabeseni ake, ndi zikho za chopereka cha chakumwa. Aikeponso buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse.

8Tsono pamwamba pa zimenezo ayalepo nsalu yofiira, ndi kuziphimba zonsezo ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mphiko m'zigwinjiri zake.

9Atenge nsalu yobiriŵira ndi kuphimba choikaponyale, pamodzi ndi nyale zake, mbaniro zake, mbale za phulusa ndi ziŵiya zake zonse za mafuta.

10Ndipo achiike pamodzi ndi zipangizo zake zonse m'thumba la zikopa zambuzi, ndi kuchiika pa chonyamulira chake.

11Ayale nsalu yobiriŵira pa guwa lagolide, ndi kuliphimba ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.

12Atenge zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito m'malo opatulika, aziike m'nsalu yobiriŵira, ndipo aziphimbe ndi zikopa zambuzi, ndi kuziika pa chonyamulira chake.

13Ataye phulusa lapaguwa, ndipo ayalepo nsalu yofiira.

14Aikepo ziŵiya zonse zapaguwa zimene amagwiritsira ntchito pamenepo, monga zofukizira lubani, zitsulo zokoŵera nyama, zoolera phulusa ndi mabeseni, kungoti ziŵiya zonse za pa guwalo. Pa zonsezo ayalepo zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.

15Tsono Aroni ndi ana ake, atamaliza kuphimba malo opatulika pamodzi ndi zipangizo zake zonse, pamene anthu akusamuka, ana a Kohati ndiwo abwere kudzanyamula zimenezi, koma asakhudze zinthu zopatulika, kuti angafe. Zimenezi ndizo zinthu za m'chihema chamsonkhano zimene ana a Kohati azinyamula.

16“Eleazara mwana wa wansembe Aroni, azisamala mafuta a nyale, lubani wonunkhira, chopereka cha chakudya choperekedwa nthaŵi zonse, ndi mafuta odzozera. Aziyang'anira malo opatulika ndi zonse za m'kati mwake, ndiponso chipinda chopatulika kwambiri ndi zipangizo zake.”

17Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,

18“Musalole kuti a m'banja la Kohati aonongeke pakati pa Alevi.

19Kuti Akohatiwo asafe, akayandikira zinthu zopatulika kopambana, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe, ndipo apatse aliyense mwa Akohatiwo zoti achite ndi zoti anyamule.

20Koma asaloŵe kukayang'ana zinthu zopatulika mpang'ono pomwe, kuti angafe.”

Za Ageresoni

21Chauta adauza Mose kuti,

22“Uŵerengenso ana a Geresoni potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

23Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano.

24Zimene mabanja a Geresoni ayenera kuchita, ndiponso zimene ayenera kumanyamula ndi izi:

25azinyamula nsalu zochinga malo opatulika, chihema chamsonkhano pamodzi ndi chophimbira chake, zikopa zambuzi zophimba pamwamba pake, ndiponso nsalu zochinga pa khomo la chihema chamsonkhano.

26Azinyamulanso nsalu zochingira bwalo, nsalu yochingira khomo la pa chipata cha bwalo lozungulira malo opatulika ndi guwa, zingwe zake ndi zipangizo zina zonse zofunika. Agwire ntchito zonse zimene aŵapatse.

27Amene aziyang'anira ntchito zonse za ana a Ageresoni, ndi Aroni pamodzi ndi ana ake. Aziyang'anira zonse zimene ayenera kunyamula, ndi zonse zimene ayenera kuchita. Ndinu amene mudzayenera kuŵafotokozera udindo wa kunyamula zonse zija.

28Imeneyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Ageresoni m'chihema chamsonkhano, ndipo woyang'anira ntchitoyo akhale Itamara, mwana wa wansembe Aroni.

Za Amerari

29“Uŵerenge ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

30Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, aliyense amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano.

31Zimene iwo alamulidwa kuti anyamule pa ntchito yao ya m'chihema chamsonkhano nazi: anyamule mitengo ya malo opatulika monga mafulemu ake, mizati yake ndi masinde ake.

32Anyamulenso mizati yozungulira bwalo, pamodzi ndi zikhomo zake, zingwe zake, kudzanso zipangizo zake zonse, ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Poŵauza zinthu zimene aliyense ayenera kunyamula, uzitchula chinthu chilichonse chimodzichimodzi.

33Imeneyi ndiyo ntchito ya mabanja a ana a Merari, ndipo ntchito yao yonse ya m'chihema chamsonkhanoyo, aziiyang'anira ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.”

Chiŵerengero cha Alevi

34Tsono Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a mpingo, adaŵerenga ana a Akohati potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

35Adaŵaŵerenga anthuwo kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano,

36ndipo chiŵerengero chao chidakwanira 2,750 potsata mabanja ao.

37Chimenecho ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'mabanja a Akohati, onse amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.

38Adaŵerenganso ana a Geresoni potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao,

39kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano.

40Chiŵerengero chao chidakwanira 2,630 potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

41Chimenechi ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'banja a Ageresoni, amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira.

42Adaŵerenganso ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao,

43kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano.

44Chiŵerengero chao chidakwanira 3,200 potsata mabanja ao.

45Ameneŵa ndiwo anthu a m'mabanja a Merari, anthu amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.

46Choncho Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele, adaŵaŵerenga Alevi onsewo potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.

47Kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kugwira ntchito yotumikira ndi yonyamula katundu wa m'chihema chamsonkhano,

48chiŵerengero chao chidakwanira 8,580.

49Anthuwo adaŵasankha kuti ena azigwira ntchito yotumikira, ndipo ena azinyamula katundu, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Umu ndimo m'mene adaŵaŵerengera anthuwo, monga momwe Chauta adaamlamulira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help