Mas. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lam'maŵa lopempha chithandizoSalmo la Davide, pamene ankathaŵa Abisalomu, mwana wake.

1Inu Chauta, ndili ndi adani ochuluka,

anthu ambiri akundiwukira.

2Anthu ambiri akamalankhula za ine amati,

“Mulungu samupulumutsa.”

3Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza,

ndinu ulemerero wanga,

mumalimbitsa mtima wanga ndinu.

4Ndimafuulira Chauta kuti andithandize,

Iye amandiyankha ali pa phiri lake loyera.

5Ndimagona ndipo ndimapeza tulo.

Ndimadzukanso m'maŵa

pakuti Chauta amanditchinjiriza.

6Sindichita mantha

ngakhale adani anga ndi osaŵerengeka,

ngakhale andizinge ndi kundithira nkhondo.

7Inu Chauta, dzambatukani,

mundipulumutse Inu Mulungu wanga.

Adani anga onse mwaŵaomba makofi,

anthu oipa mwaŵagulula mano.

8Mumatipulumutsa ndinu, Inu Chauta.

Madalitso anu akhale pa anthu anu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help