1Ku Kesareya kunali munthu wina, dzina lake Kornelio. Iyeyu anali mkulu wa asilikali 100 achiroma, a m'gulu lotchedwa “Gulu la ku Italiya.”
2Anali munthu wotsata zachipembedzo, ndipo iye pamodzi ndi banja lake lonse ankaopa Mulungu. Ankathandiza kwambiri Ayuda osauka, ndipo ankapemphera Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi.
3Tsiku lina dzuŵa litapendeka, nthaŵi ili ngati 3 koloko, adaona zinthu m'masomphenya. Adaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu akubwera kwa iye nkunena kuti, “Kornelio!”
4Iye adayang'anitsitsa mngeloyo mantha atamgwira, ndipo adamufunsa kuti, “Nkwabwino, Ambuye?” Mngeloyo adati, “Mulungu wakondwera nawo mapemphero ako ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo zako.
5Tsopano tuma anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro.
6Akukhala kwa Simoni wina, mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.”
7Mngelo amene ankalankhula naye uja atachoka, Kornelio adaitana antchito ake aŵiri, ndiponso msilikali. Msilikaliyo anali mmodzi mwa amene ankamutumikira, ndipo anali munthu wopembedza Mulungu.
8Kornelio uja ataŵafotokozera zonse, adaŵatuma ku Yopa.
9
41Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa.
42Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe.
43Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”
Anthu a mitundu ina alandira Mzimu Woyera44Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo.
45Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe.
46Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati,
47“Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?”
48Motero adalamula kuti abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.