1Tamandani Chauta.
Ndidzathokoza Chauta ndi mtima wanga wonse
pa msonkhano wa anthu olungama mtima.
2Ntchito za Chauta nzazikulu,
onse okondwera nazo amazilingalira.
3Ntchito zake ndi zaulemu ndi zaufumu,
ndipo kulungama kwake nkwamuyaya.
4Amatikumbutsa ntchito zake zodabwitsa,
Chauta ndi wokoma ndi wachifundo.
5Amapatsa chakudya anthu omuwopa,
amakumbukira chipangano chake nthaŵi zonse.
6Amaonetsa anthu ake mphamvu za ntchito zake,
poŵapatsa choloŵa cha anthu a mitundu ina.
7Ntchito za manja ake nzokhulupirika ndi zolungama.
Malamulo ake onse ndi okhulupirika.
8Ndi okhazikika mpaka muyaya,
paja adaŵapereka ndi mtima wokhulupirika ndi wolungama.
9Adapulumutsa anthu ake.
Adakhazikitsa chipangano chake
kuti chikhale chamuyaya.
Dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
10 Yob. 28.28; Miy. 1.7; 9.10 Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru.
Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni.
Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.