1Saulo adaloŵa ufumu ali ndi zaka 30, ndipo adalamulira Aisraele zaka ngati 42.
2Nthaŵi ina iye adasankha Aisraele 3,000. Mwa ameneŵa, 2,000 anali ndi Sauloyo ku Mikimasi ndi ku dziko lamapiri ku Betele, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibea m'dziko la Benjamini. Anthu ena onse otsala adaŵabweza kwao.
3Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.”
4Ndipo Aisraele onse adamva mbiri yakuti Saulo adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti, ndiponso kuti Afilisti anali ataipidwa kwambiri ndi Aisraele. Motero anthu adaitanidwa kuti abwere kwa Saulo ku Giligala.
5Tsono Afilisti adasonkhana pamodzi kuti amenyane nkhondo ndi Aisraele. Adasonkhanitsa magaleta ankhondo 30,000, okwera pa akavalo 6,000 ndi ankhondo ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Iwowo adapita nakamanga zithando zao ku Mikimasi, kuvuma kwa Betaveni.
6Pamene Aisraele adaona kuti ali m'zoopsa, poti anali atapanikizidwadi kwambiri, adakabisala m'mapanga, m'maenje, m'matanthwe, m'makwaŵa ndi m'zitsime.
7Ena adaoloka Yordani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi. Saulo anali ku Giligalabe, ndipo anthu okhala naye anali njenjenje ndi mantha.
8 1Sam. 10.8 Sauloyo adadikira masiku asanu ndi aŵiri, monga momwe adaanenera Samuele. Koma Samueleyo sadafike ku Giligala, ndipo anthu adayamba kumthaŵira Saulo uja.
9Choncho Saulo adati, “Bwera nayoni kuno nsembe yopserezayo pamodzi ndi nsembe zachiyanjano zija.” Ndipo Saulo adapereka nsembe yopsereza ija.
10Atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, adangoona Samuele watulukira. Tsono Saulo adapita kukakumana naye ndi kumulonjera.
11Samuele adamufunsa Sauloyo kuti, “Nanga nchiyaninso mwachitachi?” Iye adayankha kuti, “Pamene ndinaona kuti anthu akundithaŵira, ndipo kuti inuyo nthaŵi imene mudaanena ija simudabwere, ndiponso kuti Afilisti adasonkhana ku Mikimasi,
12ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, ine ndisanapemphe Chauta kuti andikomere mtima.’ Motero ndinadzikakamiza kupereka nsembe yopserezayi.”
13Apo Samuele adamuuza kuti, “Mwachitatu zopusa. Simudatsate zimene Chauta, Mulungu wanu, adakulamulani. Mukadazitsata, bwenzi Chauta atakhazikitsa ufumu wanu pakati pa Aisraele mpaka muyaya.
14Ntc. 13.22 Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Chauta wadzifunira yekha munthu wa kumtima kwake. Chauta wamsankha munthuyo kuti akhale mfumu yolamulira anthu ake, chifukwa inu simudatsate zimene Iye adakulamulani.”
15Atatero Samuele adanyamuka ku Giligala napita ku Gibea ku dziko la Benjamini.
Saulo akonzekera nkhondo.Saulo adaŵerenga anthu amene anali naye, ndipo adapeza kuti alipo 600.
16Tsono iyeyo ndi mwana wake Yonatani, pamodzi ndi anthu amene anali nawowo, adakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti adamanga zithando zankhondo ku Mikimasi.
17Ankhondo a Filisti adatuluka kuchoka ku zithando zao m'magulu atatu. Gulu limodzi lidalunjika ku Ofura ku dziko la Suwala.
18Gulu lina lidalunjika ku Betehoroni, ndipo lina lidalunjika ku malire oyang'anana ndi chigwa cha Zeboimu chakuchipululu.
19Nthaŵi imeneyi nkuti mulibe msuli ndi mmodzi yemwe m'dziko lonse la Israele, chifukwa Afilisti ankati, “Tisaŵalole Ahebri kuti azidzisulira okha malupanga ndi mikondo.”
20Motero Mwisraele aliyense ankapita kwa Afilisti kukasanjitsa pulao kapena khasu lake, ndi kukanoletsa nkhwangwa yake kapena chikwakwa.
21Mtengo wonoletsera nkhwangwa unali ndalama imodzi, ndipo mtengo wosanjitsira makasu ndi wosongoletsera zisonga unali ndalama ziŵiri.
22Motero tsiku lankhondolo panalibe lupanga kapena mkondo m'manja mwa Mwisraele aliyense amene ankatsata Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi mwana wake Yonatani, iwo okha ndiwo anali nazo zida.
23Tsono Afilisti adatuma kagulu kankhondo kukalonda mpata wa Mikimasi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.