1Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi a anthu ambiri,
mzinda wodzaza ndi mabodza ndi zakuba,
wokonda kufunkha mosalekeza.
2Imvani kulira kwa zikoti,
kukokoma kwa mikombero,
likitilikiti wa akavalo
ndi kulilima kwa magaleta.
3Okwera pa akavalo akuthamanga,
malupanga ali ŵaliŵali,
mikondo ili phuliphuli.
Afa anthu ambiri,
mitembo yati vuu, yosaŵerengeka,
anthu kumaphunthwa pa mitemboyo.
4Zonsezo zachitika
chifukwa cha zonyansa
zochuluka za Ninive,
mkazi wachiwerewere uja.
Ankakopa anthu ndi kukongola kwake konyenga.
Ankanyengadi anthu a mitundu yonse ndi zadama zake
nakopa mafuko ndi zithumwa zake.
5Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,
“Ine sindikugwirizana nawe,
ndidzakuvula ndi kukunyazitsa.
Anthu a mitundu yonse adzaona maliseche ako,
udzachita manyazi pamaso pa maiko onse.
6Ndidzakuthira zonyansa,
ndidzakunyodola,
ndipo ndidzakusandutsa chinthu chomachiseka.
7Ndipo onse okuwona adzakuthaŵa, adzati,
‘Ninive wasanduka bwinja,
adzamlira ndani?’
Ndidzamtenga kuti woti akusangalatse?”
Akuterotu Chauta.
8Kodi iwe Ninive ndiwe wopambana Thebesi?
Suja mzinda umenewu unali m'mbali mwa
mtsinje wa Nailo utazingidwa ndi madzi.
Madziwo anali ngati khoma lake ndi linga lake?
9Mzindawo unkalamulira Etiopiya ndi Ejipito,
mphamvu zake zinali zopanda malire.
Aputi ndi Alibiya ndiwo ankagwirizana nawo.
10Komabe anthu a ku Thebesi adagwidwa,
adasanduka akapolo.
Ana ao adaŵakankhanthitsa pansi
m'miseu yonse ya mumzindamo.
Adani adagaŵana anthu otchukawo mwamaere.
Akuluakulu onse adaŵamanga ndi maunyolo.
11Iwenso Ninive udzachita ngati waledzera,
mutu wako udzazungulira.
Nawenso udzafunafuna malo othaŵirako.
12Malinga ako onse adzakhala ngati
mitengo ya nkhuyu zoyamba kupsa.
Akaigwedeza, nkhuyuzo zimagwera m'kamwa
mwa wofuna kuzidya.
13Ankhondo ako ali ngati akazi.
Zipata za dziko lako zaŵatsekukira adani ako,
ndipo moto wapsereza mipiringidzo yake.
14Mutungiretu madzi kuti adzakwanire
pa nthaŵi yokuzingani,
limbitsani malinga anu.
Pondani dothi,
ponyani m'chikombole,
ndipo muumbe njerwa.
15Ngakhale mutero, moto udzakupserezanibe,
ndipo lupanga lidzakukanthani,
mudzapululuka ngati dzombe.
Swanani ngati dzombe,
chulukanani ngati ziwala.
16Mudachulukitsa anthu anu amalonda
kupambana nyenyezi zamumlengalenga.
Koma onsewo adamwazikana ngati dzombe.
17Nduna zanu zili ngati dzombe.
Akuluakulu anu ali ngati ziwala,
zimene zimangokangamira pa khoma kukazizira.
Koma dzuŵa likamatuluka, zimauluka,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene
amadziŵa kumene zapita.
18Iwe mfumu ya Aasiriya, nduna zako zaferatu.
Akuluakulu ako apitiratu.
Anthu ako amwazikira ku mapiri,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe woŵasonkhanitsa.
19Palibe mankhwala a bala lako,
chilonda chako sichingapole.
Onse amene amamva za iwe,
amaomba m'manja mokondwa.
Kodi alipo wina amene sadazilaŵepo
nkhanza zako zosathazi?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.