Mphu. 51 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

ZOONJEZERANyimbo yothokoza

1Ndikukuthokozani,

Inu Ambuye anga ndi mfumu yanga.

Ndikukutamandani

Mulungu Mpulumutsi wanga.

2Ndikukuthokozani,

chifukwa mudanditchinjiriza

ndi kundichirikiza.

Mudandipulumutsa ku imfa,

ku msampha wa munthu wosinjirira,

ndi ku milomo yonama bodza.

3Pamaso pa adani anga,

mudandithandiza ndi kundipulumutsa

potsata ukulu wa chifundo chanu ndi ulemerero

wa dzina lanu.

Mudandipulumutsa kwa anthu ondikukutira mano

ofuna kuti andidye,

kwa amene ankafuna kundipha,

ndi ku mavuto ambiri amene ndidapirira.

4Mudandipulumutsa ku moto umene udanditentha

mbali zonse,

ndi pakati pa moto umene sindinayatse ndine.

5Mudandipulumutsa ku manda akuya ndi ku

lilime loipa ndi lamabodza,

lilime londisinjirira kwa mfumu.

6Ndinali pafupi kufa,

moyo wanga unkakhudza manda.

7Adani adandizungulira ponseponse,

koma panalibe wondithandiza.

Ndidafunafuna chithandizo

koma osachiwona.

8Tsono ndidakumbukira chifundo chanu,

Inu Ambuye,

ntchito zanu za masiku amakedzana.

Mumaombola anthu okhulupirira Inu,

ndipo mumaŵapulumutsa kwa adani ao.

9Tsono ndidapemphera m'dziko lino lapansi,

kupempha kuti mundipulumutse ku imfa.

10Ndidapemphera kwa Ambuye,

Tate wa mbuye wanga, kuti,

“Musandisiye pa mavuto anga,

pamene ndikusoŵa chithandizo pakati pa

anthu onyada.

11Ndidzatamanda dzina lanu kosalekeza,

ndi kukuimbirani nyimbo zothokoza.”

Ndipo Inu mudamva pemphero langa.

12Paja mudandipulumutsa ku imfa,

ndi kundithandiza nditataya mtima.

Nchifukwa chake ndikukuthokozani ndi

kukuyamikani,

ndiponso ndikutamanda dzina lanu, Inu Ambuye.

13Ndikali mnyamata, ndisanayambe kuyendayenda,

ndidapemphera poyera kuti ndipeze nzeru.

14Kunja kwa Nyumba yopembedzera ndidapempha nzeru,

ndipo ndidzazifunafuna pa moyo wanga wonse.

15Kuyambira ubwana wanga mpaka ukalamba wanga

mtima wanga wakhala ukukondwerera nzeruzo.

Ndakhala ndikuzitsata kuyambira ubwana wanga,

chifukwa ndidaayamba kale kuzikonda.

16Ntangotchera khutu pang'ono ndidazilandira,

ndipo ndidaphunzira zambiri.

17Chifukwa cha nzeruzo, zanga zonse zidapita patsogolo.

Motero ndidzatamanda amene adandipatsa nzeru.

18Ndidatsimikiza kuzigwiritsa ntchito zimene

ndidaphunzira.

Ndidachita khama kufuna zabwino,

ndipo sindidzachita manyazi konse.

19Ndidafunitsitsa kupeza nzeru ndi mtima wanga wonse,

ndipo ndidachita khama kutsata Malamulo.

Tsono ndidakweza manja anga kumwamba

ndilikudandaula chifukwa cha umbuli wanga.

20Ndidaika mtima pa kufunafuna nzeru,

ndipo nditalewa machimo, ndidazipeza.

Zidandithandiza kumvetsa zinthu

kuyambira pamene ndidazipeza,

nchifukwa chake sindidzatayika.

21Mtima wanga udaafunitsitsa kuzipeza,

ndipo ndidalandiradi mphatso yaikuluyo.

22Ambuye adandipatsa mphatso ya kulankhula bwino,

ndipo ndidzamlemekeza nayo.

23Bwerani kwa ine inu amene simudaphunzire,

mudzaphunzire m'sukulu yanga.

24Chifukwa chiyani mukudandaula kuti zinthuzi zikusoŵani,

pamene moyo wanu ukuzifuna chotere?

25Paja ndidalengeza kuti,

“Muzilandire popanda kupereka ndalama.

26Longani makosi anu m'goli la nzeru,

ndipo mtima wanu ulandire maphunziro ake,

amapezeka pafupipafupi.”

27Onani ine, ndidadza thukuta pang'ono chabe,

koma ndidapeza mtendere waukulu.

28Gulani maphunziro ndi siliva wambiri,

mukatero mudzapeza golide wambiri.

29Mukondwere ndi chifundo cha Ambuye,

musachite nako manyazi kuŵatamanda.

30Gwirani ntchito yanu pa nthaŵi yoyenera,

ndipo Mulungu adzakupatsani mphotho yanu

pa nthaŵi yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help