Mphu. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mtima wako usakhulupirire chuma,

nkumanena kuti, “Ndadala!”

2Usafeŵerere zilakolako zako ndi mphamvu zako,

usamangotsatira zifuniro zoipa za mtima wako.

3Usanene kuti, “Ndani angandichite kanthu?”

Ukatero, Mulungu adzakulanga.

4 Mla. 8.11 Usanene kuti, “Ndidachimwa, koma palibe chimene chidaoneka.”

Zimenezi zingoonetsa kuti Ambuye ngopirira nthaŵi yaitali.

5Usakhulupirire udyo kuti Mulungu adzakukhululukira,

mpaka kumachulukitsa dala machimo ako.

6Usanene kuti, “Chifundo chake nchachikulu,

adzandikhululukira machimo anga, ngakhale achuluke chotani.”

Iyeyo ngwachifundodi, komanso amakwiya,

sangalephere kulanga ochimwa.

7Usazengereze kubwerera kwa Ambuye,

usamati, “Ndibwerera maŵa.”

Ukatero, mkwiyo wa Ambuye udzakugwera mwadzidzidzi,

ndipo adzakukantha pa nthaŵi ya chilango.

8Usagonere pa chuma chopata monyenga,

poti pa nthaŵi ya tsoka sichidzakuthandiza.

Za kukhala wolungama ndi wodzisunga

9Usamapete zinthu ndi mphepo iliyonse,

kapena kumangoyenda m'njira iliyonse,

monga m'mene amachitira munthu wochimwa wokamba paŵiripaŵiri.

10Uzilimbikira pa zimene udziŵa,

ndipo usamasinthesinthe mau ako.

11Uzifulumira kumvetsera,

koma usamayankha msanga.

12Munthu uzimuyankha pamene ukudziŵa chonena,

koma ngati sudziŵa, dzanja lako ligwire pakamwa.

13Kulankhula kumatha kubweretsa ulemerero kapena manyazi.

Munthu angathe kugwa ndi mau ake omwe.

14Usatchuke ndi ukazitape,

usatchere anzako misampha ndi mau ako.

Paja mbala manyazi amaigwera,

ndiponso munthu wokamba paŵiripaŵiri mlandu

umamgwera.

15Usamachite molakwa pa zinthu zazikulu ndi

zazing'ono zomwe.

Usasanduke mdani m'malo mokhala bwenzi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help