Esr. C - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero la Mordekai

1Tsono Mordekai, pokumbukira ntchito zonse zimene Ambuye adazichita, adayamba kupemphera.

2Adati, “Inu Ambuye, Ambuye, ndinu Mfumu yamphamvuzonse, zinthu zonse zili mu ulamuliro wanu. Mutafuna kupulumutsa Israele, palibe amene angakuletseni.

3Mudalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndiponso zinthu zabwino zonse za pansi pano.

4Inu ndinu mbuye wa zonse, ndipo palibe wina angathe kulimbana ndi Inu, Ambuye.

5Mumadziŵa zinthu zonse, Ambuye. Mukudziŵa kuti pamene ndinkakana kuŵeramira Hamani wodzikuza uja, si chifukwa cha mwano kapena kunyada, kapena chifukwa chofuna ulemu chabe ai.

6Chikadakhala chothandiza kupulumutsa Israele, bwenzi nditalolera kunyambita ngakhale mapazi omwe a Hamaniyo.

7Choncho chimene ndidaalekera kumuŵeramira nchakuti sindidafune kulemekeza munthu kupambana m'mene ndimalemekezera Mulungu. Sindingapembedze munthu aliyense, koma Inu nokha, Ambuye. Choncho sindidalekere kunyada ai.

8“Koma tsopano, Ambuye Mulungu, Inu Mfumu, Mulungu wa Abrahamu, mupulumutse anthu anu. Maso a adani athu ali pa ife, kufuna kutipha tonse. Akuti atiwonongeretu ife anthu anu osankhidwa chikhalire.

9Musatisiye ife anthu anu amene mudadziwombolera potitulutsa m'dziko la Ejipito.

10Ife ndife anthu anu, tsono mverani pemphero langa, ndipo mutimvere chifundo. Mavuto athu muŵasandutse chimwemwe, Inu Ambuye, kuti tikhale moyo ndipo tiimbe nyimbo zotamanda dzina lanu. Musaononge anthu amene pakamwa pao pamakutamandani.”

11Aisraele onse adalira kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse, chifukwa adaaona kuti imfa yaŵayandikira.

Pemphero la Estere

12Mfumukazi Estere nayenso, alikumva nthumanzi yoopsa, adatembenukira kwa Ambuye.

13Adavula zovala zake zokongola, navala zamaliro ndi zachisoni. M'malo modzola mafuta onunkhira, adadzola phulusa ndi ndoŵe kumutu kwake. Adaipitsa maonekedwe a thupi lake, ndipo adalekerera tsitsi lake osalipesa, kuti liphimbe thupi lake limene ankakonda kulikongoletsa.

14Tsono adapemphera kwa Ambuye, Mulungu wa Israele, kuti, “Ambuye anga, Mfumu yathu ndinu nokha. Dzandithandizeni, ndili ndekha, ndilibe wina wondithandiza, koma Inuyo basi.

15Ndili pafupi kuchita kanthu kamene kangandipezetse imfa.

16Kuyambira ndili mwana, makolo anga akhala akundiwuza kuti mudasankhula Israele pakati pa mitundu yonse ya anthu, ndipo kuti pa masiku amakedzana mudapatula makolo athu pakati pa ena onse kuti akhale anthu anuanu mpaka muyaya. Ndipo zonse zimene mudaŵalonjeza, mudazichitadi.

17Koma ife takuchimwirani, ndipo mwatipereka kwa adani athu,

18chifukwa takhala tikupembedza milungu yao. Ndinu achilungamo, Ambuye.

19Koma adani athu sakukhutira kuti ife tili mu ukapolo woopsa. Adalonjeza kwa mafano ao,

20akuti adzafafaniziratu zomwe Inu mudazilamula, ndiponso akuti adzaononga anthu anuanu. Akutinso adzaŵakhalitsa chete onse okutamandani ndi kuthetsa ulemerero wa guwa lanu ndi wa Nyumba yanu.

21Akufuna kuti anthu a mitundu yonse azitamanda mafano ao achabe ndi kumalemekeza nthaŵi zonse mfumu imene ili munthu woyenera kufa.

22“Inu Ambuye, ufumu wanu usagonje kwa mafano amene sali kanthu konse. Musalole kuti adani athu azitiseka chifukwa cha kuwonongedwa kwathu. Koma muŵagwetsere iwo omwe chiwembu chaocho, ndipo iye uja amene adayambitsa za chiwembu chotichita ifechi mumlange kwakukulu, akhale chitsanzo.

23Mutikumbukire Ambuye, ndipo mutipulumutse pa nthaŵi ino ya mavuto athu. Ineyo mundilimbitse, Inu Mfumu ya milungu yonse, Ambuye amphamvuzonse.

24Mundipatse mau oyenera amene ndikanene pamaso pa mkango uja. Sinthani mtima wake kuti adane ndi Hamani, mdani wathu uja, kuti choncho Hamaniyo pamodzi ndi gulu lake aonongedwe.

25Eks. 3.6Ambuye, dzanja lanu litipulumutse, inenso mundithandize, chifukwa ndili ndekha ndipo ndilibe wina wondithandiza koma Inu nokha.

26Inu mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ine ndimadana nazo zoti akunja azindilemekeza. Ndimanyansidwa nako kugona ndi anthu osaumbalidwa ndiponso achilendo.

27Mukudziŵa kuti amachita kundikakamiza, mwiniwakene ndimadana nacho chisoti chaufumu chimene ndimayenera kuchivala popita ku misonkhano. Chimandinyansa ngati nsanza yovala pa nthaŵi yamsambo, ndipo sindichivala pamene ndikungokhala khale.

28Ndimakana kudya nawo pa tebulo la Hamani, ndipo sindikhala nawo pa phwando la mfumu kapena kumwa nawo vinyo wake.

29Momwe ndidabwerera kuno, chimodzi chokha chimene chimandikondweretsa nkupembedza Inu Ambuye, Mulungu wa Abrahamu.

30Inu Mulungu wamphamvuzonse, mverani mapemphero a anthu anu otaya mtima. Mutipulumutse kwa anthu oipaŵa, ndipo ineyo mundichotse mantha.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help