1“Kodi iwe umaidziŵa nthaŵi imene zinkhoma zimaswera?
Kodi udaziwonapo nswala zikubadwa?
2Kodi ungathe kuŵerenga miyezi imene zimakhala ndi bele?
Kodi nthaŵi imene nyamazi zimaswa iwe umaidziŵa?
3Kodi ukuidziŵa nthaŵi
imene zidzakhala tsonga nkuswa ana, kenaka nkutayiza?
4Ana a nyamazi amakhala amphamvu, namakulira ku thengo.
Pambuyo pake amapita, osabwereranso kwa mai wao.
5“Kodi abulu akuthengo adaŵapatsa ndani
ufulu wongodziyendera?
Ndani adaŵapatsa liŵilo lao?
6Ine ndidaŵapatsa chipululu
kuti chikhale malo ao okhalako,
ndiponso chichere kuti chikhale dera lao.
7Amakhala kutali ndi mizinda yaphokoso,
ndipo sadziŵa mau okuwa a anthu
oyendetsa nyama zakatundu.
8Kumapiri ndiko kumene kuli busa lao.
Kumene amafunafuna msipu woti adye.
9“Kodi njati ingavomere kukutumikira?
Kodi ingagone m'khola mwako usiku?
10Kodi ungathe kuimanga ndi nsinga kuti izilima?
Kodi ingasalaze nthumbira m'munda mwako?
11Kodi ungadalire njatiyo chifukwa cha mphamvu zake?
Kodi ungayembekeze kuti ikugwirira ntchito yako?
12Kodi ungakhulupirire kuti
idzabwera nkudzatuta tirigu wako ku malo opunthira?
13“Nthiŵatiŵa ikukupiza mapiko ake monyadira,
koma nthenga zake ndi mapiko ake
sizikuithandiza kuuluka monga amachitira kakoŵa.
14Nthiŵatiŵa imafotsera mazira ake pansi,
kuti afundidwe m'nthaka.
15Koma imaiŵala kuti mapazi ake omwe
angathe kuphwanya mazirawo,
ndipo kuti nyama zakuthengo nkuŵapondereza.
16Nthiŵatiŵa imachita ana ake nkhalwe ngati si ake.
Zakuti idaavutika poŵabereka imaiŵalako.
17Paja Mulungu adaimana nzeru,
kotero kuti simvetsa kanthu kalikonse.
18Komabe nthiŵatiŵayo ikadzambatuka nkuyamba kuthaŵa,
imamsiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.
19“Kodi ndiwe amene umapatsa mphamvu kavalo?
Nanga ndiwe amene umaveka chenjerere m'khosi mwake?
20Kodi ndiwe amene umamlumphitsa ngati dzombe?
Kavalo akamadzuma, mpweya wake
ndi waukali ndiponso woopsa.
21Kavaloyo amalumphalumpha m'chigwa,
ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.
22Sachita mantha, sachita nkhaŵa,
ndipo sabwerera m'mbuyo akaona lupanga.
23Zida zankhondo za wokwerapo wake
zimachita kwichikwichi m'phodo,
ndipo mkondo ndi nthungo zimanyezemira pa dzuŵa.
24Akavalowo amanjenjemera ndi ukali
nathamangira kutsogolo,
ndipo akangomva lipenga sangathe kuima.
25Lipenga likalira amati, ‘Twee!’
Amamva fungo la nkhondo ali patali.
Amamva kufuula kwa atsogoleri ankhondo.
26“Kodi ndi nzeru zako
zimene zimaphunzitsa kabaŵi kuuluka,
ndi kutambalitsa mapiko ake kupita chakumwera?
27Kodi umalamula chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka?
Kodi udachiphunzitsa ndiwe kukamanga chisa
pamwamba penipeni?
28Chimakhala pa phiri, nkumanga chisa chake pamenepo,
pansonga penipeni pa thanthwe losakwereka.
29Pamenepo chimayang'ana choti chigwire kuti chidye,
ndipo maso ake amachiwonera patali chinthucho.
30 Mt. 24.28; Lk. 17.37 Ana ake amayamwa magazi,
amapezeka kumene kuli mitembo.”
Kuyankha kwa Yobe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.