Ntc. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 M'buku langa loyamba lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi,

2kufikira tsiku limene adatengedwa kupita Kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adaŵasankha aja zoti iwowo adzachite.

3Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adaŵaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai.

4 ndiponso Yudasi (mwana wa Yakobe.)

14Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

15Tsiku lina, patapita masiku angapo, Petro adaimirira pakati pa abale. (Anthuwo onse pamodzi anali ngati 120.) Iye adati,

16“Abale anga, kunayenera kuti zichitikedi zimene Malembo adaneneratu za Yudasi. Paja kudzera mwa Davide Mzimu Woyera adalankhula za iyeyo amene adatsogolera anthu okagwira Yesu.

17Yudasiyo anali mmodzi wa gulu lathu, ndipo adaalandira udindo woti azitumikira pamodzi ndi ife.

18 pochita chosalungama chija. Kumeneko adagwa chamutu, naphulika pakati, matumbo ake onse nkukhuthuka.

19Anthu onse okhala ku Yerusalemu adamva zimenezi, kotero kuti m'chilankhulo chao mundawo adautcha dzina loti ‘Akeledama,’ ndiye kuti, ‘Munda wa Magazi.’

20 mpaka tsiku limene adatengedwa kuchoka pakati pathu kupita Kumwamba. Mmodzi mwa anthu ameneŵa akhale mboni pamodzi ndi ife, yakuti Yesu adauka kwa akufa.”

23Pamenepo iwo adatchula maina aŵiri: Yosefe amene ankamutcha Barsabasi (dzina lake lina ndi Yusto,) ndi Matiasi.

24Ndipo adapemphera kuti, “Ambuye, Inu amene mumadziŵa mitima ya anthu onse, tiwonetseni ndi uti mwa aŵiriŵa amene mwamusankha

25kuti alandire ntchito iyi ya utumwi, m'malo mwa Yudasi uja amene adaisiya ndipo adapita ku malo omuyenera.”

26Tsono adaŵachitira maere anthu aŵiriwo. Maerewo adagwera Matiasi, ndipo iyeyo adawonjezedwa pa gulu lija la atumwi khumi ndi mmodzi.

Blog
About Us
Message
Site Map