1Wansembe Pasuri, mwana wa Imeri, amene anali kapitao wamkulu ku Nyumba ya Chauta, adamva Yeremiya akulosa zinthu zimenezi.
2Tsono Pasuri adalamula kuti anthu amenye mneneri Yeremiya ndi kumuika m'ndende ku chipata cha Benjamini, ku Nyumba ya Chauta.
3M'maŵa mwake Pasuri adatulutsa Yeremiya m'ndende, ndipo Yeremiya adauza Pasuri kuti, “Chauta sakutchulanso dzina loti Pasuri, koma loti ‘Zoopsa pa mbali zonse.’
4Paja Chauta akunena kuti: Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe, ndiponso kwa abwenzi ako onse. Abwenzi akowo adani ao adzaŵapha ndi lupanga, iweyo ukupenya. Ndipo Yuda yense ndidzampereka kwa mfumu ya ku Babiloni. Ena adzaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni, ndipo ena adzaŵapha ndi lupanga.
5Chuma chonse chamumzindamu, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zonse za mtengo wapatali ndi chuma cha mafumu a ku Yuda, zonsezo ndidzazipereka kwa adani ao. Iwowo adzafunkha zimenezi ndi kupita nazo ku Babiloni.
6Ndipo iwe Pasuri ndi onse a pabanja pako, nanunso adzakutengani ukapolo kupita nanu ku Babiloni. Mudzafera komweko ndi kuikidwa komweko, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unkaŵalosera zabodza.”
Yeremiya adandaula kwa Chauta7Inu Chauta, mwandipusitsa ine,
ndipo ndapusadi.
Inu ndinu amphamvu kuposa ine,
ndipo mwandipambana.
Aliyense akundiseka tsiku lonse,
aliyense akundinyodola kosalekeza.
8Ndikamalankhula, ndimakweza mau,
ndimafuula kuti, “Ndeu kuno, taonongeka!”
Mau anu, Inu Chauta, andisandutsa wonyozeka
ndi wonyodoledwa masiku onse.
9Ndikanena kuti, “Sindidzalalikanso za Chauta,
sindidzalankhulanso m'dzina lake,”
mau anu, Inu Chauta, amayaka ngati moto
mumtima mwanga.
Ndimayesa kuŵasunga m'kati,
koma pambuyo pake ndimaŵatulutsa
popeza kuti sindingathe kupirira.
10Ndimamva ambiri akunong'ona.
Zoopsa zili pa mbali zonse! Amati,
“Kamnenezeni! Tiyeni tikamneneze!”
Amene adaali abwenzi anga amayembekeza kuti
ndigwa pansi, amati,
“Mwina mwake adzatha kunyengedwa,
tsono ife tidzamgwira ndi kulipsira pa iyeyo.”
11Koma Chauta ali nane, ndiye wankhondo woopsa.
Nchifukwa chake anthu ondizunza adzakhumudwa,
ndithu sadzandipambana.
Adzachita manyazi kwambiri, chifukwa cha kundilepherako,
ndipo manyazi aowo sadzaiŵalika konse.
12Inu Chauta Wamphamvuzonse,
amene mumaweruza anthu molungama,
amene mumapenya zamumtima,
ndikupereka mlandu wanga kwa Inu.
Ndikukupemphani kuti mundilipsirire adani anga.
13Imbirani Chauta, mtamandeni Chauta!
Ndiye amapulumutsa osauka kwa adani ao.
14 Yob. 3.1-19 Litembereredwe tsiku limene ndidabadwa.
Lisatamandidwe tsiku limene mai wanga adandibala.
15Tsoka kwa iye
amene adakasangalatsa bambo wanga ndi uthenga woti,
“Kunyumba kwanu kwabadwa mwana wamwamuna.”
16Munthu ameneyo akhale ngati mizinda
imene adaiwononga Chauta mopanda chifundo ija.
Amve kulira kwa kupweteka m'maŵa,
ndiponso phokoso la nkhondo masana,
17chifukwa choti sadandiphere m'mimba,
kuti mai wanga asanduke manda anga,
ndipo kuti mimba yake ikhale chitupire.
18Kodi chifukwa chiyani ndidabadwa?
Kodi ndidabadwira mavuto ndi chisoni,
kuti moyo wanga ukhale wa manyazi okhaokha?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.