1“Ine tsono pa chaka choyamba cha ufumu wa Dariusi Mmedi, ndidaimirira kuti ndimlimbikitse ndi kumchirikiza.
Nkhondo pakati pa Ejipito ndi Siriya2“Tsopano ndikuuza zoona. Ku Persiya kudzakhala mafumu ena atatu. Pambuyo pake padzakhala yachinai, yolemera kwambiri kupambana ena onsewo. Idzakhalanso yamphamvu chifukwa cha chuma chakecho. Idzautsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi.
3Tsono kudzaoneka mfumu ina yamphamvu. Imeneyo idzalamulira ufumu waukulu, ndipo idzachita zimene ikufuna.
4Koma ufumu wake utafika pake penipeni, udzaonongeka, ndipo udzagaŵikana panai. Sudzaolokera ku zidzukulu zake, ndipo oloŵa m'malo mwake sadzakhala ndi mphamvu zonga zake. Ufumu wake udzazulidwa ndi mizu yomwe, ndipo udzapatsidwa kwa ena, osati kwa iwo aja.
5“Mfumu yakumwera idzakhala yamphamvu. Koma wina mwa akalonga ake adzaipambana pa mphamvu, ndipo ulamuliro wake udzakhala waukulu kwambiri.
6Patapita zaka zingapo mafumu aŵiri, yakumpoto ndi yakumwera, adzachita chipangano. Mwana wamkazi wa mfumu yakumwera adzabwera kudzakwatiwa ndi mfumu yakumpoto kuti akhazikitse mtendere. Koma ufumuwo sudzakhalitsa ai, mfumuyo ndi ana ake sadzakhalitsa. Mkaziyo, mwamuna wake, mwana wake, ndi atumiki ake, onsewo adzaperekedwa kwa adani.
7Pambuyo pake mmodzi mwa achibale a mkaziyo adzaloŵa ufumu. Iyeyu adzathira nkhondo mfumu yakumpoto. Adzaigonjetsa nkuloŵa mumzinda mwake.
8Adzatenga zofunkha kubwerera nazo ku Ejipito pamodzi ndi mafano a milungu yao, ndiponso ziŵiya za mtengo wapatali zagolide ndi zasiliva. Tsono pa zaka zina zingapo adzaleka kumenyana ndi mfumu yakumpotoyo.
9Pambuyo pake mfumu yakumpoto ija idzaloŵanso ndi nkhondo m'dziko la mfumu yakumwera, koma idzalephera nkubwerera ku dziko lake.
10“Ana a mfumu yakumpoto adzaputa nkhondo nadzasonkhanitsa asilikali ambirimbiri. Onsewo adzabwera ngati chigumula nadzathira nkhondo ufumu wakumwera mpaka kukafika ku malinga a mfumu.
11Apo mfumu yakumwera idzatuluka mokwiya kukamenyana nayo nkhondo mfumu yakumpotoyo ndi gulu lake lankhondo lalikulu zedi, ndipo idzaligonjetsa.
12Gulu lankhondo limeneli litagwidwa, mfumu yakumwerayo idzayamba kudzikuza chifukwa cha kupambana kwake, ndipo idzapha anthu zikwi zambiri. Komabe kupambanako sikudzapitirira.
13“Mfumu yakumpotoyo idzasonkhanitsanso gulu lankhondo lalikulu kupambana lakale. Patapita zaka zingapo idzabwera ndi gulu lankhondo lalikululo ndi zida zambiri zankhondo.
14Masiku amenewo anthu ambiri adzaipandukira mfumu yakumwera. Anthu ena andeu mwa anthu ako nawonso adzaukira ufumuwo, kuti achitedi zimene zidaoneka m'masomphenyazo, koma adzalephera.
15Tsono mfumu yakumpoto idzafika, idzazinga mzinda ndi nthumbira zankhondo, ndipo idzaugwira mzinda wamalingawo. Asilikali ankhondo akumwera sadzalimbika, ngakhale ankhondo ake amphamvu omwe adzalephera.
16Tsono mdani wakumpotoyo adzachita monga akufuna, ndipo palibe amene adzalimbane naye. Adzakhazikika m'maiko abwino kwambiriwo, ndipo zonse zidzakhala mu ulamuliro wake.
17“Kenaka mfumu yakumpotoyo idzabwera ndi mphamvu zake zonse, nidzayesa kupangana za mtendere ndi mfumu yakumwera. Idzayesa kupereka mwana wake kwa mfumu inayo kuti imkwatire, koma cholinga chake sichidzagwira ntchito konse.
18Pambuyo pake mfumu yakumpotoyo idzathira nkhondo maiko a m'mbali mwa nyanja ndipo idzagonjetsa ambiri. Koma mtsogoleri wina wankhondo adzathetsa kudzikuza kwake. Motero chipongwe chakecho chidzaibwerera.
19Mfumuyo idzayesa kubwerera ku malinga a dziko lake, koma idzaphunthwa, nkugwa, osapezekanso.
20“Pambuyo pa mfumu imeneyi padzaoneka mfumu ina imene idzatuma wokhometsa msonkho kuti chuma cha ufumu wake chichuluke. Koma patapita kanthaŵi pang'ono mfumuyo idzaphedwa, osati mwaukali kapena pa nkhondo ai.
Mfumu yoipa yakumpoto21“M'malo mwake mudzaloŵa munthu wonyozeka, wosakhala wa m'banja lachifumu. Iyeyo adzangobwera mwadzidzidzi, ndipo adzalanda ufumuwo monyengerera.
22Adzapirikitsa ndi kutheratu magulu ankhondo, ngakhalenso wansembe wa chipangano.
23Ndipo kuyambira nthaŵi imene adzachite naye chipangano, adzachita zinthu monyenga. Ngakhale kuti adzakhale ndi anthu ochepa, adzakhala ndi mphamvube.
24Mwadzidzidzi adzathira nkhondo madera olemera kwambiri a dzikolo. Motero adzatha kuchita zimene makolo ake ndi makolo a atate ake sadathe kuchita. Adzagaŵa zofunkha, zolanda ndiponso chuma pakati pa anthu omutsata. Adzakonzekera kugwira mizinda yamalinga, koma zimenezi zidzachitika pa kanthaŵi pang'ono chabe.
25“Mfumu yakumpoto idzalimba mtima ndi kusonkhanitsa gulu lankhondo lamphamvu kwambiri, kuti ikamenyane ndi mfumu yakumwera. Koma mfumu yakumwerayo idzamenyana nayo nkhondo ilinso ndi gulu lalikulu kopambana, koma sidzapambana, chifukwa adzaichita chiwembu.
26Ngakhale aphungu ake odya naye pamodzi adzamuukira. Gulu lake lankhondo lidzaonongeka, ndipo ambiri adzaphedwa pa nkhondoyo.
27Pambuyo pake mafumu aŵiriwo adzakhala pa tebulo limodzi, koma mitima yao idzakhala yonyenga, ndipo adzanamizana. Koma sadzaphulapo kanthu, chifukwa nthaŵi idzakhala isanafike.
28Tsono mfumu yakumpoto idzabwerera kwao ili ndi katundu wambiri, koma mtima wake udzafunitsitsa kuwononga chipembedzo cha anthu a Mulungu. Idzachita monga ifunira, ndipo idzabwerera kwao.
29“Patapita nthaŵi, mfumu yakumpoto idzabwereranso kumwera, koma sidzapambana monga idaachitira kale.
30Zombo za ku maiko akuzambwe zidzalimbana nayo, ndipo iyoyo idzataya mtima. Pamenepo idzabwerera ili yopsa mtima kwabasi, ndipo idzachichita zoipa chipembedzo. Idzavomerezana nawo anthu amene asiya kale chipembedzocho.
31Ankhondo ake adzaipitsa malo amalinga a m'Nyumba ya Mulungu, ndipo adzathetsa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku. Kumeneko adzaikako Chonyansa chosakaza chija.
32Mfumuyo idzachita zinthu moshashalika, kuti ikope anthu onyoza kale chipembedzo chao. Koma anthu amene amadziŵa Mulungu wao adzalimbikira ndipo adzaikana mfumuyo.
33Amene ali anzeru pakati pa anthuwo adzaphunzitsa anzao ambiri. Koma patapita kanthaŵi adzaphedwa ndi lupanga ndi moto, ndipo adzafunkhidwa ndi kutengedwa ukapolo.
34Anthuwo akuzunzidwa choncho, ena adzaŵathandiza, koma ambiri othandizawo adzakhala onyenga.
35Ena mwa anzeruwo adzaphedwadi, koma cholinga chake cha zimenezi ndi kuŵayesa, kuŵayeretsa ndi kuŵakometsa mpaka nthaŵi yomaliza, pakuti idzafika nthaŵi yomwe Mulungu adaika.
36“Mfumu yakumpotoyo idzachita zimene ikufuna ndipo idzadzikuza ndi kudziyesa yaikulu kupambana milungu yonse, ngakhale Mulungu wa milungu. Zonse zidzaiyendera bwino mpaka itakwana nthaŵi imene Mulungu adzailanga mwamkwiyo, chifukwa zimene zatsimikizika zidzachitikadi.
37Mfumuyo idzanyoza milungu ya makolo ake ndiponso mulungu wokondedwa ndi akazi. Sidzasamala mulungu wina aliyense, chifukwa idzadzikuza kupambana onse.
38M'malo mwake idzalemekeza mulungu woteteza malinga, amene makolo ake sadamudziŵe. Idzapereka kwa mulunguyo golide ndi siliva, miyala ya mtengo wapatali, ndiponso mphatso zabwino kwambiri.
39Idzalimbitsa malinga ake ndi chithandizo cha anthu opembedza mulungu wachilendo. Oitumikira idzaŵalemekeza kwambiri. Idzaŵapatsa ulamuliro pa anthu ambiri, ndipo idzaŵagaŵira dzikolo ngati malipiro.
40“Pa nthaŵi yotsiriza, mfumu yakumwera idzathira nkhondo mfumu yakumpotoyo. Koma mfumu yakumpoto idzaithamangira mwaukali ngati mphepo yamkuntho, ili ndi magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi zombo zambiri. Tsono idzaloŵa m'maiko ambiri, nidzaŵakokolola ngati chigumula cha madzi.
41Idzathira nkhondo dziko lokongola kwambiri, ndipo idzapha anthu zikwi zambiri. Koma Aedomu ndi Amowabu ndiponso akulu a Aamoni adzapulumuka.
42Idzathira nkhondo maiko ambiri, ndipo ngakhale Ejipito sadzapulumuka.
43Mfumuyo idzalanda chuma cha golide ndi siliva, ndiponso zinthu za mtengo wapatali za ku Ejipito. Nawonso a ku Libiya ndi Etiopiya adzagonja kwa mfumuyo.
44Koma mbiri zochokera kuvuma ndi kumpoto zidzaiwopsa, ndipo idzanyamuka ili yokwiya kwambiri kuti ikaononge ndi kuŵatheratu anthu ambiri.
45Idzamanga mahema ake aufumu pakati pa nyanja ndi pa phiri pamene pamangidwa Nyumba ya Mulungu. Komabe potsiriza pake mfumuyo idzaphedwa popanda woithandiza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.