Aef. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kuyenda m'kuŵala

1Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira.

2Eks. 29.18; Mas. 40.6Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

3Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.

4Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu.

5Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.

6Munthu wina aliyense asakupusitseni ndi mau onyenga, pakuti zinthu zotere ndizo zimadzetsa ukali wa Mulungu pa anthu omupandukira.

7Nchifukwa chake musamagwirizane nawo anthu otere.

8Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala.

9Pajatu pamene pali kuŵala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse.

10Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye.

11Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse.

12Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi.

13Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera.

14Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati,

“Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa,

ndipo Khristu adzakuŵalira.”

15Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru.

16Akol. 4.5Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.

17Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.

18Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.

19Akol. 3.16, 17Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.

20Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

Za akazi ndi amuna m'banja

21Inu amene mumaopa Khristu, muzimverana.

22 Akol. 3.18; 1Pet. 3.1 Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga mumamvera Ambuye.

23Paja mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, monga momwe Khristu ali mutu wa Mpingo, umene uli thupi lake, ndipo Iye mwini ndi Mpulumutsi wa Mpingowo.

24Tsono monga Mpingo umamvera Khristu, momwemonso akazi azimvera amuna ao pa zonse.

25 Akol. 3.19; 1Pet. 3.7 Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.

26Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake.

27Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu.

28Momwemonso amuna azikonda akazi ao, monga momwe eniakewo amakondera matupi ao. Amene amakonda mkazi wake, ndiye kuti amadzikonda iye yemwe.

29Palibiretu munthu amene amadana ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamala bwino, monga momwe Khristu amachitira Mpingo wake.

30Amatero chifukwa Mpingowo ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo zake.

31Gen. 2.24Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.”

32Mau ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo.

33Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help