1 Yer. 49.36; Dan. 7.2; Zek. 6.5 Pambuyo pake ndidaona angelo anai ataimirira pa mbali zinai za dziko lapansi. Anali atagwira mphepo zinai za dziko lapansi kuti ndi imodzi yomwe isaombe pa dziko, kapena pa nyanja, kapena pa mtengo uliwonse.
2Kenaka ndidaona mngelo wina akukwera kuchokera kuvuma, ali ndi chidindo cha Mulungu wopatsa moyo. Mokweza mau adafuulira angelo anai aja amene Mulungu adaaŵapatsa mphamvu yoonongera dziko ndi nyanja.
3Ezek. 9.4, 6Adaŵauza kuti, “Musaononge msanga dziko, kapena nyanja, kapenanso mitengo, tiyambe taŵalemba chizindikiro pa mphumi atumiki a Mulungu wathu.”
4Tsono ndidamva chiŵerengero cha olembedwa chizindikiro aja. Chidakwanira zikwi 144, ndipo olembedwa chizindikirowo anali a m'fuko lililonse la Aisraele.
5Olembedwa chizindikiro:
A m'fuko la Yuda anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Rubeni anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Gadi anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
6A m'fuko la Asere anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Nafutali anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Manase anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
7A m'fuko la Simeoni anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Levi anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Isakara anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
8A m'fuko la Zebuloni anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Yosefe anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
A m'fuko la Benjamini anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
Za chinamtindi cha anthu ochokera m'mitundu yonse9 2Es. 2.42 Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona chinamtindi cha anthu osaŵerengeka. Anthuwo anali ochokera m'mitundu yonse ya anthu, ndi m'mafuko onse, ndipo anali a zilankhulo zonse. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Mwanawankhosa uja; anali atavala mikanjo yoyera, nthambi zakanjedza zili m'manja.
10Ankafuula mokweza mau kuti, “Chipulumutso nchochokera kwa Mulungu wathu wokhala pa mpando wachifumu, ndiponso kwa Mwanawankhosa.”
11Angelo onse adaimirira kuzungulira mpando wachifumu uja, kuzunguliranso Akuluakulu aja ndi Zamoyo zinai zija. Angelowo adadzigwetsa chafufumimba patsogolo pa mpando wachifumuwo, napembedza Mulungu.
12Adati, “Amen! Mulungu wathu alandire matamando, ulemerero, nzeru, chiyamiko, ulemu, mphamvu ndi nyonga mpaka muyaya. Amen.”
13Pamenepo mmodzi mwa Akuluakulu aja adandifunsa kuti, “Kodi ovala mikanjo yoyeraŵa ndani, ndipo achokera kuti?”
14Dan. 12.1; Mt. 24.21; Mk. 13.19Ine ndidati, “Mbuyanga, mukudziŵa ndinu.” Ndipo iye adandiwuza kuti, “Ameneŵa ndi amene adapambana m'masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa.
15“Nchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu,
ndipo amampembedza m'Nyumba mwake usana ndi usiku.
Wokhala pa mpando wachifumu uja
adzakhala ngati hema lao loŵateteza.
16 Yes. 49.10 Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu.
Sadzaombedwanso ndi dzuŵa kapena kusauka ndi kutentha.
17 Mas. 23.1; Ezek. 34.23; Mas. 23.2; Yes. 49.10; Yes. 25.8 Pakuti Mwanawankhosa uja
amene ali pakatikati pa mpando wachifumu,
adzakhala Mbusa wao,
adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.
Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.