Mphu. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Pajatu mbiri yoipa imabweretsa manyazi ndi chidzudzulo.

Zimenezi ndizo zimene zimagwera anthu ochimwa

okamba paŵiripaŵiri.

2Usadzitame chifukwa cha maganizo ako,

kuwopa kuti mtima wako ungaphulike ngati wa nkhunzi.

3Udzayoyola masamba ako ndi zipatso zako,

ndiye udzakhala wekha ngati mtengo wouma.

4Mtima woipa umaononga mwiniwake yemweyo,

ndipo adani ake amamseka.

Za chibwenzi

5Mau abwino amachulukitsa abwenzi,

munthu wolankhula mofatsa, anthu ambiri

amamuyankha mwaulemu.

6Amene umayanjana nawo azikhala ambiri,

koma wokulangiza akhale mmodzi yekha

mwa anthu 1,000.

7Ukapala bwenzi,

uyambe wamuwona m'mene aliri;

usayambe nkumukhulupirira msanga.

8Pali ena okhala abwenzi ako

pamene zikuŵakomera,

m'menemo pa nthaŵi ya mavuto amakuthaŵa.

9Abwenzi ena amasanduka adani,

mpaka kukuchititsa manyazi poulula mikangano

imene udachita nawo.

10Pali abwenzi ena ongokonda kudzadya nawe,

koma pa nthaŵi ya mavuto safuna kukuyandikira.

11Ukakhala wolemera amakhala anzako,

kumakuthandiza kulamula antchito ako.

12Koma ukasauka amakufulatira,

amakuzemba, iwe osaŵaonanso.

13Uzikhala kutali ndi adani ako,

ndipo uzikhala mochenjera ndi abwenzi ako.

14Abwenzi okhulupirika ndi ngaka yolimba,

aliyense wopeza abwenzi otere wapeza chuma.

15Abwenzi okhulupirika ngamtengowapatali,

kukoma kwao sikungagulike ndi ndalama.

16Abwenzi okhulupirika ali ngati mankhwala opatsa moyo.

Oopa Ambuye ndiwo amene amapeza abwenzi otere.

17Munthu woopa Ambuye amakhala ndi abwenzi abwino,

monga m'mene aliri iyeyo,

abwenzi akenso ali momwemo.

Za kuphunzira luntha

18Mwana wanga, ufunefune malangizo ukadali mwana,

ndipo mpaka kukalamba, uzidzapeza ndithu luntha.

19 Yak. 5.7, 8 Uchite khama kuphunzira luntha,

monga munthu amene akulima ndi kufesa mbeu,

motero udzayembekeza phindu lalikulu.

Pofunafuna lunthalo udzapeza mavuto pa kanthaŵi,

koma posachedwa udzadya zipatso zake.

20Luntha limakhala ngati lovuta kwambiri kwa

munthu wopanda mwambo,

wopusa sakhalitsa nalo.

21Lidzamlemera zedi ngati chimwala choyesera mphamvu,

ndipo sadzakhalira kulitaya.

22Mpake kuti amati luntha,

chifukwa si anthu ambiri amalipeza.

23Mvetsa mwana wanga, ndipo uvomere malangizo anga,

usakane uphungu wanga.

24Ika miyendo yako m'matangadza a luntha,

ndipo usunge khosi lako m'goli lake.

25Ŵerama kuti ulisenze paphewa pako,

ndipo usatope nazo nsinga zake.

26Ulisunge ndi mtima wako wonse,

ndipo utsate njira zake ndi mphamvu zako zonse.

27Ulilondole ndi kulifunafuna,

ndipo lidzadziwonetsa kwa iwe;

tsono ukaligwira, usalitaye.

28Potsiriza pake lidzakupatsa mpumulo,

ndipo lidzasanduka chimwemwe kwa iwe.

29Matangadza ake adzakutchinjiriza kwambiri,

ndipo goli lake lidzakhala ngati chovala chaulemu.

30Goli lake lidzakhala ngati chokongoletsera chagolide,

ndipo nsinga zake zidzakhala ngati chigwe chobiriŵira.

31Udzalivala ngati chovala chaulemu,

ndipo pamutu pako lidzakhala ngati nsangamutu yachimwemwe.

32Mwana wanga, ngati ufuna, udzaphunziradi.

Ngati uikapo mtima, udzakhala waluntha.

33Ngati ukonda kumvetsera udzaphunzira,

ngati utchera khutu, udzakhala waluntha.

34Ukakhale pakati pa anthu aakuluakulu,

ukakaona wina waluntha,

ukaphatikane ndi ameneyo.

35Umvetsere mokondwa

mau onse okamba za Mulungu,

malangizo aluntha asamakupite.

36Ukapeza munthu waluntha

uzifulumira kukakamba naye,

phazi lako lifumbule pakhomo pake.

37 Yos. 1.8; Mas. 1.2 Uzisinkhasinkha mau a Ambuye,

uzilingalira malamulo ake nthaŵi zonse.

Ndiwo amene adzakuunikira nzeru zako,

ndipo luntha limene umalifuna udzalipeza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help