2 Mbi. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumukazi ya ku Sheba ibwera kudzachezera kwa Solomoni(1 Maf. 10.1-13)

1 Mt. 12.42; Lk. 11.31 Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali. Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima mwake.

2Solomoni adayankha mafunso ake onse. Panalibe kanthu kalikonse kobisika kwa Solomoniyo, kamene sadathe kuimasulira mfumukaziyo.

3Tsono itaona nzeru zonse za Solomoni, nyumba imene adaamanga ija,

4chakudya cha patebulo pake, m'mene zinkakhalira nduna zake, m'mene ankasungira mwambo atumiki ake ndi zovala zao, atumiki ake operekera zakumwa ndi zovala zao, ndiponso nsembe zake zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Chauta, mfumukaziyo idangoti kukamwa pululu, kusoŵa chonena.

5Pamenepo idauza mfumu Solomoni kuti, “Zimene ndinkamva ndili kudziko la kwathu zonena za ntchito zanu ndi nzeru zanu, nzoonadi.

6Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndikuona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiuzeko zonse ngakhale ndi theka lomwe la nzeru zanu zonse. Mukupambana kutali mbiri imene ndidaaimva.

7Ngodala anthu anu. Ngodala atumiki anuŵa, amene amaima pamaso panu nthaŵi zonse nkumamva nzeru zanu.

8Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando wake waufumu, kuti mukhale mfumu yotumikira Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adakulongani ufumu kuti muzilamulira Aisraele, chifukwa choti Mulungu wanu adakonda Israele mpaka muyaya, nafuna kuti akhalepo mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yake yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.”

9Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zonunkhira zambirimbiri ndiponso miyala yamtengowapatali. Nkale lonse sikudaoneke zokometsera chakudya zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni.

10Komanso anyamata a mfumu Hiramu pamodzi ndi anyamata a Solomoni amene adaabwera ndi golide wa ku Ofiri, adabweranso ndi mitengo ya mbawa ndi miyala yamtengowapatali.

11Ndipo mitengo ya mbawayo mfumu idasanjira makwerero a ku Nyumba ya Chauta ndi a ku nyumba ya mfumu. Ndipo anthu oimba nyimbo adaŵapangira apangwe ndi azeze, amene kunalibe nkale lonse ku dziko la Yuda.

12Tsono Solomoni adapatsa mfumukazi ya ku Sheba ija zonse zimene inkafuna ndiponso chilichonse chimene idaapempha, osaŵerengera zimene anali ataipatsa kale posinthana nayo mphatso. Tsono mfumukaziyo idabwerera ku dziko lakwao pamodzi ndi atumiki ake aja.

Chuma cha mfumu Solomoni(1 Maf. 10.14-25)

13Golide amene ankabwera kwa Solomoni pa chaka chimodzi ankakwanira makilogramu 23,000,

14osaŵerengera amene ankabwera ndi anthu amalonda. Mafumu onse a ku Arabiya pamodzi ndi nduna zam'dzikomo ankabwera ndi siliva ndi golide kwa Solomoni.

15Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu pafupi asanu ndi aŵiri.

16Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira makilogramu atatu. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni.

17Mfumu idapangitsanso mpando waukulu waufumu wa minyanga yanjovu niwukuta ndi golide weniweni.

18Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi okafikirapo, ndiponso chopondapo mapazi, zonsezo zagolide. Mpandowo unali ndi zogwirira ndi zosanjikapo manja uku ndi uku, ndiponso zifanizo ziŵiri za mikango iŵiri itaima pambali pa zosamizapo manjazo.

19Panalinso mikango pa mbali zonse ziŵiri za kwerero lililonse, mikango khumi ndi iŵiri yonse pamodzi. Mpando sudapezekepo mu ufumu wina uliwonse.

20Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide, ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Siliva sanalinso kanthu pa nthaŵi ya Solomoni.

21Mfumu inali ndi zombo zimene zinkapita ku Tarisisi ndi anyamata a mfumu Huramu, ndipo chaka chachitatu chilichonse, zombo za ku Tarisisi zinkabwera ndi golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi.

22Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru.

23Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi ankafunafuna kuti amuone Solomoni ndi kumva nzeru zake zimene Mulungu adaaika mumtima mwake.

24Aliyense mwa iwo ankabwera ndi mphatso zake, zinthu zasiliva ndi zagolide, zovala, zida zankhondo, zokometsera chakudya, akavalo ndi abulu. Ndipo zimenezi zinkachitika choncho chaka ndi chaka.

251Maf. 4.26 Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zosungiramo akavalo ndi magaleta ake, ndiponso anthu 12,000 okwera pa akavalo. Adaŵaika ena ku mizinda yokhalako ankhondo, ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu.

26Gen. 15.18; 1Maf. 4.21 Tsono ankalamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, mpakanso ku malire a ku Ejipito.

27Ndipo ku Yerusalemu mfumuyo idasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mikungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.

28Deut. 17.16 Akavalo ankaŵaitanitsa ku Ejipito ndi ku maiko onse, kugulira Solomoni.

Solomoni amwalira

29Tsono ntchito zina zonse za Solomoni kuyambira pa chiyambi mpaka kumaliza, paja zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la ulosi wa Ahiya wa ku Siloni, ndiponso m'buku lokamba zimene mneneri Ido adaziwona m'masomphenya zokhudza Yerobowamu mwana wa Nebati.

30Solomoni adalamulira Aisraele onse ku Yerusalemu zaka makumi anai.

31Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide bambo wake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help