2 Ako. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kupereka zachifundo

1 Aro. 15.26 Abale, tifuna kuti mudziŵe za m'mene Mulungu adadalitsira mipingo ya ku Masedoniya.

2Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi.

3Ine ndikuŵachitira umboni kuti adapereka monga adathera, ngakhalenso mopitirira pamenepo poyerekeza ndi chuma chao.

4Popanda wina aliyense woŵakakamiza adatipempha, natiwumiriza kuti tiŵapatse mwai woti nawonso athandize anthu a Mulungu a ku Yudeya.

5Ndipo adathandizadi mopitirira pa zimene tidaayembekeza, pakuti poyamba adadzipereka kwa Ambuye, kenaka mwa kufuna kwa Ambuye adadziperekanso kwa ife.

6Nchifukwa chake tidaapempha Tito kuti akatsirizenso pakati panu ntchitoyi yakusonkhanitsa zopereka zachifundo imene iye anali atayamba kale.

7Zonse mudalandira pakulu, monga kukhulupirira, kulankhula, kudziŵa zinthu, kuchita changu pa zonse, ndiponso kutikonda. Motero tifuna kuti muperekenso pakulu zachifundozi.

8Pamene ndikunena zimenezi, sindikuchita kulamula ai. Pakukufotokozerani za changu cha ena, ndingofuna kuwona ngati chikondi chanu ndi chikondi chenicheni.

9Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.

10Pa nkhani imeneyi maganizo anga ndi akuti nkwabwino kuti mutsirize zimene mudayamba kale chaka chathachi, osati kungofuna kuzichita, komanso kuzichita kumene.

11Tiyeni tsono muzitsirize. Paja munali ndi changu pofuna kuzichita, muchitenso changu tsopano kuzitsiriza molingana ndi zimene muli nazo.

12Malinga munthu akakhala ndi changu cha kupereka, Mulungu amalandira mokondwa zimene munthuyo ali nazo, ndipo samkakamiza kuti apereke zimene alibe.

13Sindikufuna kunena kuti inuyo muvutike, ena apepukidwe, ai, koma kuti pakhale kulingana.

14Poti inu muli ndi zambiri tsopano, muyenera kumathandiza osoŵa, kuti m'tsogolomo nawonso akadzakhala ndi zochuluka, azidzakuthandizani pa zosoŵa zanu. Motero padzakhala kulingana.

15Eks. 16.18 Paja Malembo akuti,

“Amene adapata zambiri, sizidamchulukire,

amene adapata pang'ono, sizidamchepere.”

Za Tito ndi anzake

16Tiyamike Mulungu kuti adaika mumtima mwa Tito changu chomwecho chimene ife tili nacho pokuthandizani.

17Pakuti sadangochita zimene tidampempha, koma changu chake chinali chachikulu, kotero kuti adatsimikiza yekha zobwera kwanuko.

18Pamodzi ndi iyeyo tikutuma mbale wathu uja, amene mipingo yonse ikumuyamika chifukwa cha ntchito yake yolalika Uthenga Wabwino.

19Ndipo si pokhapo ai, komanso mipingo idamsankha kuti adzatiperekeze pokapereka zopereka zachifundozi. Tikukonza zimenezi kuti tichitire Ambuye ulemu, ndiponso kuti tiwonetse mtima wathu wofuna kuthandiza.

20Sitikufuna kupatsa anthu chifukwa choti azitinenera zoipa pa mayendetsedwe athu a zopereka zachifundo zochulukazi.

21Miy. 3.4Ifetu tikufuna kuchita zabwino, osati pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

22Pamodzi ndi iwowo tikutuma mbale wathu wina. Takhala tikumuyesa kaŵirikaŵiri, ndipo tampeza kuti ndi wachangu ndithu pa zinthu zambiri. Tsopano akufunitsitsa koposa kuti athandize, popeza kuti amakukhulupirirani kwambiri.

23Kunena za Tito, iyeyu ndi wantchito mnzanga amene amagwirizana nane pokuthandizani. Kunenanso za abale athu enawo, ngotumidwa ndi mipingo, ndipo Khristu amalemekezedwa chifukwa cha iwo.

24Tsono muŵatsimikizire chikondi chanu, kuti mipingo yonse ichiwone, ndi kudziŵa kuti sitikulakwa tikamakunyadirani.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help