1 Maf. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Munda wamphesa wa Naboti

1Panali munthu wina wa ku Yezireele dzina lake Naboti. Iyeyo anali ndi munda wamphesa ku Yezireele, pafupi ndi nyumba ya mfumu Ahabu.

2Tsiku lina, Ahabu adauza Naboti kuti, “Tandipatsa munda wakowu kuti ukhale dimba langa, poti uli pafupi ndi nyumba yanga. M'malo mwake ndidzakupatsa wina wabwino koposa, kapena ngati ufuna, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawo.”

3Koma Naboti adauza Ahabu kuti, “Ndithu, pali Chauta, sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.”

4Apo Ahabu adakaloŵa m'nyumba mwake atakwiya, msunamo uli toloo chifukwa cha zimene Naboti wa ku Yezireele adaanena, pakuti adaati, “Sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.” Motero Ahabu adakagona pabedi pake atapenya ku khoma, osafuna ndi kudya komwe.

5Koma Yezebele, mkazi wake uja, adabwera kwa iye namufunsa kuti, “Chifukwa chiyani nkhope yanu ikuwoneka yosakondwa, ndipo simukufuna chakudya?”

6Ahabu adauza mkazi wakeyo kuti, “Chifukwa chake nchakuti ine ndinakamba ndi Naboti wa ku Yezireele ndi kumuuza kuti andipatse munda wake wamphesawu kuti ndigule, kapena ngati afuna, ndidzamupatse munda wina m'malo mwake. Koma iyeyo wayankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wamphesawu.’ ”

7Apo Yezebele mkazi wakeyo adamufunsa kuti, “Kodi mfumu ya ku Israele sindinu? Dzukani, kadyeni, mtima wanu usangalale. Ine ndidzakutengerani munda wamphesawo kwa Naboti wa ku Yezireele.”

Naboti aphedwa.

8Tsono Yezebele adalemba makalata m'dzina la Ahabu, naŵasindikiza ndi chidindo cha mfumu. Adatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa atsogoleri amene ankakhala ndi Naboti mumzinda mwake.

9M'makalatamo adalembamo kuti, “Lalikani kuti anthu asale zakudya, ndipo Naboti amuike pa malo aulemu.

10Mupeze anthu aŵiri oipa mtima kuti adzamneneze ndi mau akuti, ‘Iwe watemberera Mulungu ndiponso mfumu.’ Tsono mumtulutsire kunja, ndipo mumponye miyala kuti afe basi.”

11Motero anthu a mumzinda m'mene ankakhala Nabotiyo, akuluakulu ndi atsogoleri amumzindamo, adachitadi monga momwe adaaŵauzira Yezebele. Potsata mau am'makalata omwe mkaziyo adaŵatumizira,

12anthuwo adalengeza za kusala zakudya, ndipo adamuika Naboti pa malo aulemu.

13Anthu aŵiri aja adaloŵa nakhala pamaso pa Nabotiyo. Adayamba akuchita umboni pakhamu pa anthu onse kuti, “Nabotiyu adatemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Motero anthuwo adamtulutsira kunja kwa mzinda, namponya miyala mpaka kumupha.

14Pambuyo pake adatumiza mau kwa Yezebele akuti, “Naboti uja takonza, moti wafa.”

15Yezebele atangomva zakuti Naboti amponya miyala ndipo wafa, adakauza Ahabu kuti, “Dzukani, katengeni munda wamphesa uja umene Naboti Myezireele, ankakukanizani kugula. Nabotiyo sali moyonso ai, wafa.”

16Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, adanyamuka napita ku munda wamphesa wa Naboti Myezireele, nautenga kuti ukhale wake.

Eliya auza Ahabu kuti banja lake lonse lidzaonongeka.

17Pambuyo pake Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti,

18“Nyamuka, pita ukakumane ndi Ahabu, mfumu ya ku Israele, amene akukhala ku Samariya. Iyeyu ali ku munda wamphesa wa Naboti. Wapita kumeneko kuti akatenge mundawo kuti ukhale wake.

19Tsono ukamuuze kuti Chauta akukufunsa kuti, ‘Kodi wapha, ndipo walandanso?’ Ukamuuzenso kuti, ‘Chauta akunena kuti, pa malo amene agalu ankanyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako.’ ”

20Apo Ahabu adafunsa Eliya kuti, “Kani wandipeza, iwe mdani wanga?” Eliya adayankha kuti, “Ee, ndakupezani, chifukwa inuyo mwadzigulitsa ndi kukhala ngati kapolo wa zoipa zochimwira Chauta.

21Tsopano Chauta akuti, ‘Ndithu, ndidzakupasula. Ndidzakusesa kwathunthu, ndidzaononga mwamuna aliyense pa banja lako, kapolo kapena mfulu, m'dziko la Israele.

22Ndipo banja lako ndidzalisandutsa kuti likhale ngati banja la Yerobowamu mwana wa Nebati, ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. Nawenso wandikwiyitsa, chifukwa chakuti wachimwitsa anthu a ku Israele’

232Maf. 9.36 Tsono kunena za Yezebele, Chauta akuti agalu adzamudya Yezebele m'kati mwa malinga a Yezireele.

24Munthu aliyense wa banja la Ahabu amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Ndipo aliyense wa banja limenelo wodzafera ku thengo, mbalame zamumlengalenga ndizo zidzamudye.”

25Kunena zoona kunalibe ndi mmodzi yemwe amene adadzipereka ku zoipa kuchimwira Chauta ngati Ahabu, amene Yezebele mkazi wake adamkopa.

26Iyeyo adachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga m'mene ankachitira Aamori aja, amene Chauta adaŵachotsa pamene Aisraele ankafika.

27Ahabu atamva mau amenewo, adang'amba zovala zake, navala ziguduli. Adasala zakudya nagona pa zigudulizo, ndipo adayamba kuyenda modzichepetsa.

28Apo Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti,

29“Kodi waona m'mene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, sindidzamlanga ndi zonse zija iyeyo ali moyo. Koma ndidzalanga banja lake, kuyambira mwana wake.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help