1 Pet. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndine, Petro, mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa inu osankhidwa a Mulungu, amene muli obalalikira ku chilendo, ku maiko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya ndi Bitiniya.

2Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira.

Za chiyembekezo chenicheni

3Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima

42Es. 8.52kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.

5Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.

6Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zoŵaŵa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthaŵi.

72Es. 16.73Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.

8Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka.

9Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.

10Aneneri amene adaneneratu za mphotho yaulere imene mudzalandireyo, ankafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi.

11Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo ankaneneratu za zoŵaŵa zimene Khristu adzamve, ndiponso za ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake. Aneneriwo ankafunafuna kudziŵa kuti kodi zimenezi zidzachitika liti, ndiponso mwa njira yanji.

12Mulungu adaŵaululira kuti ntchito yaoyi sankaigwira chifukwa cha eniakewo, koma chifukwa cha inu, pamene iwo ankanena zoonazi zimene mwamva tsopano. Olalika Uthenga Wabwino adakuuzani zoonazi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera Kumwamba. Angelo omwe amalakalaka kuwona nao zinthuzo.

Aŵapempha kuti ayesetse kukhala oyera mtima

13Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke.

14Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa.

15Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse.

16Lev. 11.44, 45; 19.2 Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”

17Mulungu alibe tsankho. Amaweruza aliyense molingana ndi zochita zake. Ngati mumutcha Atate pamene mukupemphera, mchitireni ulemu nthaŵi yonse muli alendo pansi pano.

18Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai,

19adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.

20Iyeyo Mulungu adaamsankhiratu dziko lapansi lisanalengedwe, koma wamuwonetsa nthaŵi yotsiriza ino chifukwa cha inu.

21Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.

22Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti muzikondana ndi akhristu anzanu mosanyenga. Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse, mosafookera.

23Pakuti mwa mwachita kubadwanso, moyo wake si wochokera m'mbeu yotha kuwonongeka, koma m'mbeu yosatha kuwonongeka. Mbeuyi ndi mau a Mulungu, mau amoyo ndi okhala mpakampaka.

24Yes. 40.6-8 Paja mau a Mulungu amanena kuti,

“Anthu onse ali ngati udzu,

ulemerero wao uli ngati duŵa lakuthengo.

Udzu umauma, ndipo duŵa limathothoka,

25koma mau a Ambuye ngokhala mpaka muyaya.”

Mau ameneŵa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help