1 Yoh. 1.1 Tikukulemberani za Iye uja amene adaalipo kuyambira pa chiyambi, amene tidamumva ndipo tidamuwona ndi maso athu, amene tidampenya ndithu, ndipo tidamkhudza ndi manja athu: Iyeyo ndiye Mau opatsa moyo.
2Yoh. 1.14Moyowo udaoneka, ndipo ife tidauwona. Tikuuchitira umboni, ndipo tikukulalikirani za moyo wosatha, umene unali kwa Atate ndipo udatiwonekera.
3Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
4Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu.
Mulungu ndiye kuŵala5Uthenga umene tidamva kwa Iye, ndipo timaulalika kwa inu, ndi wakuti Mulungu ndiye kuŵala, ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.
6Tikanena kuti timayanjana naye, pamene tikuyendabe mu mdima, tikunama, ndipo zochita zathu nzosagwirizana ndi zoona.
7Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
8Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga, ndipo mwa ife mulibe choona.
9Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
10Tikanena kuti sitidachimwe, tikumuyesa wonama Mulungu, ndipo mau ake sali mwa ife.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.