Yer. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kalata yolembera anthu a ku ukapolo

1 2Maf. 24.12-16; 2Mbi. 36.10 Yeremiya adatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu yopita kwa atsogoleri amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri, ndi anthu ena onse amene Nebukadinezara adaaŵatenga ukapolo ku Yerusalemu kupita nawo ku Babiloni.

2Zimenezi zidachitika pamene Yehoyakini ndi mfumukazi, nduna za mfumu ndi akuluakulu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu, ndiponso anthu aluso ndi osula, anali atachoka ku Yerusalemu.

3Yeremiya kalatayo adapatsira Elasa mwana wa Safani, ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya ku Yuda adaaŵatuma ku Babiloni kwa mfumu Nebukadinezara. M'kalatamo adaalembamo kuti,

4“Anthu onse a ku Yerusalemu, amene adatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuŵauza kuti,

5‘Mangani nyumba, muzikhalamo. Limani minda, mudye zipatso zake.

6Mukwatire, ndipo mubale ana aamuna ndi ana aakazi. Ana aamunawo muŵasankhire akazi, ana aakaziwo muŵasankhire amuna, kuti abale ana aamuna ndi ana aakazi. Ndipo muchulukane kumeneko, osachepa.

7Muzikometsa ku mizinda kumene ndidakupirikitsirani ku ukapoloko, kuti zonse zizikuyenderani bwino. Muzipempherera mizindayo kwa Chauta, chifukwa choti mizindayo ikakhala pa mtendere, inunso mudzakhala pabwino.

8Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Aneneri asakunyengeni, ngakhale oombeza amene ali pakati panu, ndipo musamvere maloto ao.

9Ndithu amakuloserani zabodza m'dzina langa, Ine sindidaŵatume,’ ” akutero Chauta.

10 2Mbi. 36.21; Yer. 25.11; Dan. 9.2 Chauta akunena kuti, “Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri ku Babiloni, ndidzakuyenderani ndi kuchitadi zimene ndidakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano.

11Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

12Nthaŵi imeneyo mudzandiitana ndi kumanditama mopemba, ndipo ine ndidzakumverani.

13Deut. 4.29; Lun. 6.12, 13 Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse,

14mudzandipezadi,” akuterotu Chauta. “Ndidzakubwezerani zabwino zanu, ndi kukusonkhanitsani kuchokera ku mitundu ina ya anthu ndi kumalo konse kumene ndidakupirikitsirani. Ndidzakubwezerani kumalo kumene mudaali, ndisanakutumizeni ku ukapolo.”

15Inu mumanena kuti, “Chauta adatipatsa aneneri athu ku Babiloni.”

16Koma Chauta alipo ndi mau pa za mfumu imene ikukhala pa mpando waufumu wa Davide, ndi pa za anthu onse okhala mu mzinda uno, ndiye kuti anzanu a m'dzikomo amene sadatengedwe nao ukapolo.

17Akunena kuti, “Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri. Ndidzaŵasandutsa ngati nkhuyu zoola kwambiri, zosatinso nkudyeka ai.

18Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri, ndipo ndidzaŵasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa ndi ochititsa mantha, oŵaseka ndi onyozeka, pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene ndidaŵapirikitsira.

19Izi zidzatero chifukwa sadamvere mau anga, pamene Ine ndidakhala ndikuŵatumizira aneneri, atumiki anga. Koma inunso simudamvere,” akuterotu Chauta.

20“Nchifukwa chake tsono inu akapolo nonse amene ndidakutengani ukapolo kuchoka ku Yerusalemu kupita ku Babiloni, mverani mau a Ine Chauta.

21“Chauta Wamphamvuzonse wanenapo mau pa za Ahabu mwana wa Kalaya, ndi za Zedekiya mwana wa Maseiya, amene ankakuloserani zabodza m'dzina la Chautayo. Akuti, Ndidzaŵapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzaŵapha inu mukupenya.

22Chifukwa cha anthu aŵiriwo, maina ao azidzaŵatchula anthu a ku Yuda okhala ku Babiloni potemberera anzao. Azidzati, ‘Chauta achite nawe monga m'mene adachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu amene mfumu ya ku Babiloni adaŵatentha!’

23Zoonadi makhalidwe ao ku Israele analidi oipa, ankachita chigololo ndi akazi a eniake, ankalosa zabodza m'dzina langa, Ine osaŵalamula. Ine ndikuzidziŵa, ndingathe kuzichitira umboni zimenezi,” akuterotu Chauta.

Kalata ya Semaya

24Semaya wa ku Nehelamu ukamuuze kuti,

25“Mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndi aŵa akuti: Iweyo udatumiza kalata m'dzina lako kwa anthu onse a ku Yerusalemu, kwa Zefaniya wansembe mwana wa Maseiya, ndi kwa ansembe onse. M'kalatamo udanena kuti

26Chauta wakuika iwe Zefaniya, kuti ukhale wansembe m'malo mwa wansembe Yehoyada. Wakuika kuti ukhale kapitao woyang'anira Nyumba ya Chauta. Uzimponya m'ndende ndi kumuveka goli munthu aliyense wamsala amene amadziyesa mneneri.

27Nanga chifukwa chiyani tsono sudamchite zimenezi Yeremiya wa ku Anatoti, amene amakhala ngati mneneri pakati panu?

28Ifetu ku Babiloni kuno Yeremiyayo watitumizira mau akuti: Ukapolo wanu ukhala wautali. Mangani nyumba zoti muzikhalamo, ndipo limani minda kuti muzidya zipatso zake.”

29Kalata ya Semayayo wansembe Zefaniya adaiŵerengera pamaso pa mneneri Yeremiya.

30Tsono Chauta adauza Yeremiya kuti,

31“Utume uthenga kwa akapolo onse, uŵauze mau a Chauta onena za Semaya wa ku Nehelamu, akuti, Semaya wakuloserani, ngakhale sindidamtume, ndipo wakunyengani kuti muzikhulupirira zabodza.

32Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti: Ndidzamlanga Semaya pamodzi ndi zidzukulu zake. M'banja lakelo palibe munthu amene adzakhale pakati pa mtundu uno wa anthu, amene adzaone zabwino zomwe ndidzachitira anthu anga, chifukwa iyeyo walalika zondipandukira,” akuterotu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help