Num. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aisraele agonjetsa Akanani

1 Num. 33.40 Mfumu Yachikanani ya ku Aradi imene inkakhala kumwera, itamva kuti Aisraele akubwera, kudzera njira ya ku Atarimu, idathira nkhondo Aisraelewo, nigwirako ena ukapolo.

2Tsono Aisraele adalumbira kwa Chauta kuti, “Ngati muŵapereka anthu ameneŵa m'manja mwathu, ife tidzaonongeratu mizinda yao.”

3Chauta adamvera mau a Aisraelewo naŵaperekadi Akanani aja m'manja mwao. Aisraele adaŵaonongeratu Akananiwo pamodzi ndi mizinda yao yomwe. Choncho malowo adaŵatcha kuti Horoma.

Njoka yamkuŵa

4 Deut. 2.1 Aisraele adanyamuka ku phiri la Horo nadzera njira ya ku Nyanja Yofiira, kuzungulira dziko la Edomu. Koma pa njira adayamba kunyong'onyeka.

51Ako. 10.9Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.”

6Tsono Chauta adatumiza njoka za ululu wonga moto pakati pa anthu aja, ndipo zidaŵaluma, kotero kuti Aisraele ambiri adafa.

7Ndipo anthu adabwera kwa Mose, namuuza kuti, “Pepani tidachimwa poti tidakangana ndi Chauta ndi inu nomwe. Mupemphere kwa Chauta kuti atichotsere njokazi.” Choncho Mose adaŵapempherera anthuwo.

8Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Upange njoka yamkuŵa, ndipo uipachike pa mtengo. Aliyense wolumidwa akangoiyang'ana njokayo, adzakhala moyo.”

92Maf. 18.4; Yoh. 3.14 Choncho Mose adapanga njoka yamkuŵa, naipachika pa mtengo. Ndiye ankati wina aliyense njoka ikamuluma, munthuyo akayang'ana njoka yamkuŵa ija, ankakhala moyo.

Za ulendo wa ku chigwa cha dziko la Mowabu

10Aisraele adanyamukanso, nakamanga mahema ao ku Oboti.

11Ndipo adachoka ku Oboti nakamanga ku Iyeabarimu m'chipululu choyang'anana ndi Mowabu, kuvuma.

12Atachoka kumeneko, adakamanga m'chigwa cha Zeredi.

13Kuchokera kumeneko adakamanga patsidya pa mtsinje wa Arinoni umene uli m'chipululu chochokera ku malire a dziko la Amori. Mtsinje wa Arinoni umene ndiwo malire a Mowabu, uli pakati pa dziko la Mowabu ndi dziko la Amori.

14Nchifukwa chake buku la nkhondo za Chauta limanena kuti,

“Mzinda wa Waheba uli ku Sufa,

ku zigwa za Arinoni,

15ku matsitso a zigwa amene afika mpaka ku Ari,

nakhudza malire a dziko la Mowabu.”

16Kuchokera kumeneko adapitirira mpaka ku malo oti Beeri. Chimenecho chinali chitsime chimene Chauta adaalozera Mose namuuza kuti, “Uŵasonkhanitse pamodzi anthuwo, ndipo ndidzaŵapatsa madzi.”

17Tsono Aisraele adaimba nyimbo iyi yakuti,

“Tulutsa madzi ako, chitsime iwe,

ife tiŵaimbira nyimbo!

18Chitsime chimene adakumba mafumu,

chimene atsogoleri omveka a anthu adakumba,

adakumba ndi ndodo zao zaufumu

ndiponso ndi ndodo zao zoyendera.”

Kuchokera kuchipululu, Aisraele adafika ku Matana,

19kuchokera ku Matana adafika ku Nahaliyele, kuchokera ku Nahaliyele adafika ku Bamoti.

20Kuchokera ku Bamoti adafika ku chigwa cha m'dziko la Mowabu, kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, loyang'anana ndi chipululu cham'munsi.

Aisraele agonjetsa mfumu Sihoni ndi mfumu Ogi(Deut. 2.26—3.11)

21Tsono Aisraele adatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, kukanena kuti,

22“Mutilole kuti tidzere m'dziko mwanumo. Sitidzadzera m'minda mwanu, kapena m'mipesa mwanu. Sitidzamwa madzi a m'chitsime chanu. Tidzangotsata mseu wanu waukulu mpaka titadutsa dziko lanulo.”

23Koma Sihoni sadalole kuti Aisraele adutse dziko lake. Adasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi, napita kukamenyana nkhondo ndi Aisraele kuchipululu, ndipo adafika ku Yahazi, namenyana ndi Aisraele.

24Ndipo Aisraele adamgonjetsa ndi lupanga, nalanda dziko lake kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki, kufikira m'malire a dziko la Aamori, chifukwa malirewo anali otchinjirizidwa.

25Aisraele adalanda mizinda yonseyi nakhala m'mizinda yonse ya Aamori, ku Hesiboni ndi m'midzi yake yonse.

26Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, amene adaamenyana ndi mfumu yakale ya Amowabu, ndipo adamlanda dziko lake lonse mpaka ku mtsinje wa Arinoni.

27Nchifukwa chake oimba ndakatulo amati,

“Bwerani ku Hesiboni,

mzindawu umangidwenso,

tiyeni timange mzinda wa Sihoni

kuti ukhazikikenso.

28 Yer. 48.45, 46 Moto udabuka ku Hesiboni.

Malaŵi a moto adatuluka mu mzinda wa Sihoni.

Moto udaononga Ari mzinda wa ku Mowabu,

udapserezeratu mapiri a kumtunda kwa Arinoni.

29Tsoka kwa iwe Mowabu,

mwatha inu anthu opembedza Kemosi.

Ana ake aamuna waasandutsa othaŵathaŵa,

ana ake aakazi waasandutsa akapolo,

akapolo a Sihoni mfumu ya Aamori.

30Choncho zidzukulu zao zidatha nkufa,

kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Diboni,

ndipo tidaŵaononga mpaka ku Nofa,

pafupi ndi Medeba.”

31Motero Aisraele adakhala m'dziko la Aamori.

32Mose adatuma anthu kuti akazonde Yazere. Ndipo Aisraele adagwira midzi yake, napirikitsa Aamori amene anali kumeneko.

33Tsono adabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Ogi mfumu ya ku Basaniko adatuluka kukalimbana nawo. Iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse adakamenyana nawo nkhondo ku Ederei.

34Koma Chauta adauza Mose kuti, “Usamuwope. Ndampereka m'manja mwako pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake lomwe. Ndipo umchite zomwe udachita Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni.”

35Choncho Aisraele adapha Ogi, ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalira, ndipo adalanda dziko lakelo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help