1Ndimathaŵira kwa Inu Chauta,
musalole kuti ndichite manyazi,
koma mundipulumutse
chifukwa ndinu Mulungu wolungama.
2Tcherani khutu kuti mundimve,
fulumirani kudzandipulumutsa.
Mukhale thanthwe langa lothaŵirako,
ndi linga langa lolimba londipulumutsa.
3Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Tsogolereni ndi kundiwongolera
chifukwa Inu ndinu Chauta.
4Onjoleni mu ukonde umene anditchera,
pakuti Inu ndinu pothaŵira panga.
5 Lk. 23.46 Ndikupereka moyo wanga m'manja mwanu.
Inu Chauta wokhulupirika, mwandiwombola.
6Inu mumadana ndi opembedza mafano achabechabe.
Koma ine ndimakhulupirira Inu Chauta.
7Ndidzakondwa ndi kusangalala
chifukwa ndinu a chikondi chosasinthika.
Mwaona masautso anga,
mwazindikira mavuto anga kuti ndi aakulu.
8Simudandipereke m'manja mwa adani anga,
koma mwandiika pa malo otambalala.
9Tsono mundikomere mtima, Inu Chauta,
pakuti ndili m'zovuta.
Maso anga atupa chifukwa cha chisoni.
Mumtima mwanga ndi m'thupi momwe mwadzaza zovuta.
10Moyo wanga ukutha chifukwa cha chisoni,
zaka zanganso zikutha chifukwa cha kulira kwambiri.
Mphamvu zanga zatheratu chifukwa cha kulakwa kwanga,
mafupa anga agooka.
11Adani anga onse amandinyodola,
anzanga omwe amandiyesa chinthu chonyansa.
Anthu odziŵana nawo amandiyesa chinthu choopsa.
Anthu ondiwona mu mseu amandithaŵa.
12Andiiŵala kotheratu ngati munthu wakufa.
Ndasanduka ngati chiŵiya chosweka.
13Zoonadi, ndimamva anthu ambiri
akunong'onezana zoipa za ine,
zoopsa zandizinga ponseponse.
Amapangana zoti andiwukire,
namachita upo woipa woti andiphe.
14Koma ndimadalira Inu Chauta,
ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.”
15Masiku anga ali m'manja mwanu.
Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.
16Yang'aneni mtumiki wanune mwa kukoma mtima kwanu,
pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
17Inu Chauta, musalole kuti ndichite manyazi,
chifukwa ndapemphera kwa Inu.
Koma anthu oipa ndiwo achite manyazi,
apite ku manda kachetechete.
18Onse onyada ndi onama
olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino,
muŵakhalitse chete.
19Ndi waukulu ubwino wanu
umene mwaŵasungira anthu okumverani,
umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu,
aliyense waona zimenezi.
20Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu,
kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao.
Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza,
kuti anthu angakangane nawo.
21Atamandike Chauta:
wandiwonetsa modabwitsa chikondi chake chosasinthika,
pamene ndinali mu mzinda
wozingidwa ndi gulu la ankhondo.
22Ndidalankhula mwankhaŵa kuti,
“Andipirikitsira kutali ndi Inu.”
Koma Inu mudamva kupempha kwanga
pamene ndidakudandaulirani kuti mundithandize.
23Kondani Chauta, inu nonse anthu oyera mtima.
Chauta amasunga anthu okhulupirika,
koma amalanga koopsa anthu odzikuza.
24Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima,
inu nonse okhulupirira Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.