Yud. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nebukadinezara ndi Arifaksade

1Pa chaka cha 12 cha ufumu wa Nebukadinezara, mfumu ya Aasiriya, amene likulu lake linali ku mzinda waukulu wa Ninive, Arifaksade ankalamulira Amedi ku Ekibatana.

2Arifaksade ndiye adazinga mzinda wa Ekibatana ndi malinga a msinkhu wa mamita 30, ndi mamita 22 kuchindikira kwake pa maziko. Malingawo adaŵamanga ndi miyala yosema ya masentimita 260 kutalika kwake, ndi masentimita 130 kuchindikira kwake.

3Pa zipata za mzinda adamangapo nsanja zazitali zankhondo za msinkhu wa mamita 44, ndi mamita 26 kuchindikira kwake pa maziko.

4Zipatazo zinali za msinkhu wa mamita 30, ndi mamita 18 m'mimba mwake, kuti gulu lake lonse lankhondo lizitulukapo bwino, ngakhale asilikali oyenda pansi ali pa mizere.

5Tsono mpa masiku amenewo pamene mfumu Nebukadinezara adakamenyana nkhondo ndi Arifaksade m'chigwa chachikulu m'malire a Ragesi.

6Pamodzi ndi Arifaksade panalinso anthu onse okhala m'dziko lamapiri ndi anthu a m'mbali mwa Yufurate, Tigrisi ndi Hidaspesi, ndiponso anthu akuchigwa, olamulidwa ndi Ariyoki, mfumu ya Aelimi. Motero mafuko ambiri adadzagwirizana nawo Ababiloni.

7Tsono Nebukadinezara, mfumu ya Aasiriya, adatumiza mithenga kwa anthu onse a ku Persiya ndi onse akuzambwe. Adaitana anthu aŵa: a ku Silisiya, a ku Damasiko, a ku Lebanoni, a ku Antilebanoni ndi onse okhala m'mbali mwa nyanja yaikulu;

8a ku Karimele, Giliyadi, Galileya wakumpoto, ndi a ku chigwa chachikulu cha Esdreloni;

9onse okhala ku Samariya ndi ku mizinda yozungulira, ndi kutsidya kwa Yordani mpaka ku Yerusalemu, Betaniya, Kelusi, Kadesi, mpakanso ku mtsinje wa ku Ejipito. Enanso amene adaŵaitana ndi aŵa: anthu a ku Tapanesi ndi Ramsesi ndiponso okhala m'dziko la Goseni, ngakhale kubzola Tanisi ndi Memfisi,

10ndiponso nzika zonse za ku Ejipito mpaka ku malire a Etiopiya.

11Koma anthu a m'maiko onsewo sadausamale mthenga wa Nebukadinezara, mfumu ya Aasiriya, onse adakana kumthandiza pa nkhondo. Sankamuwopa konse, ankangoti ali yekhayekha. Choncho amithenga akewo adaŵabweza chimanjamanja, mochititsanso manyazi.

12Tsono onsewo mfumu Nebukadinezara adaŵapsera mtima kwambiri, nalumbira kuti pali mpando wake waufumu adzaŵalipsira. Adatsimikiza kuti adzaŵapha onse okhala ku Silisiya, Damasiko, Siriya, Mowabu, Amoni, Yudeya ndi Ejipito, mpaka m'mphepete mwa nyanja yaikulu ndi nyanja ya ku Persiya.

13Pa chaka cha 17 cha ufumu wake, Nebukadinezara adatuma ankhondo ake kuti akamenyane ndi mfumu Arifaksade, ndipo adampambana pa nkhondoyo. Adagonjetseratu gulu lake lonse lankhondo ndiponso okwera pa akavalo ndi a pa magaleta omwe.

14Adalanda mizinda yake, nakafika ku Ekibatana nkugwetsa nsanja zake zonse. Adafunkha misika yake yonse, naononga kotheratu kukongola kwake konse.

15Arifaksade adamgwirira ku mapiri a Ragesi. Adambaya ndi mkondo naononga kotheratu ufumu wake.

16Pambuyo pake Nebukadinezara adatenga zofunkha nabwerera ku Ninive, iyeyo pamodzi ndi ankhondo ake ndi onse amene adaadzamthandiza, gulu lalikuludi la ankhondo. Tsono adapumula kumeneko namachita madyerero pamodzi ndi gulu lake lankhondo, pa masiku 120.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help