Yes. 55 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta achitira chifundo anthu osauka

1 Chiv. 21.6; 22.17 Chauta akunena kuti,

“Inu nonse omva ludzu,

bwerani, madzi ali pano.

Ndipo inu amene mulibe ndalama,

bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye.

Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka,

osalipira ndalama, osalipira chilichonse.

2 Mphu. 24.19-22 Chifukwa chiyani ndalama zanu

mukuwonongera zinthu zimene saadya?

Chifukwa chiyani malipiro anu

mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala?

Mvetsetsani zimene ndikunena Ine,

ndipo muzidya zimene zili zabwino,

muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.

3 Ntc. 13.34 Tcherani makutu, ndipo mubwere kwa Ine.

Mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo.

Ndidzachita nanu chipangano chosatha,

ndipo ndidzakuwonetsani chikondi

chosasinthika ndi chosapeneka,

chimene ndidaalonjeza Davide.

4“Mudziŵe kuti iye uja ndidamsankha

kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu,

kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira anthu ambiri.

5Tsopano mudzaitana mitundu imene simuidziŵa.

Mitundu imene sikudziŵani idzabwera ndi liŵiro

kuti ikhale nanu,

chifukwa cha Ine Chauta, Mulungu wanu,

Woyera uja wa Israele,

amene ndidakupatsani ulemerero.”

6“Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka,

mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.

7Oipa asiye makhalidwe ao oipa,

ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa.

Abwerere kwa Chauta,

kuti Iyeyo aŵachitire chifundo.

Abwerere kwa Mulungu wathu,

kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”

8Chauta akunena kuti,

“Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi,

ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi.

9Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi,

momwemonso zochita zanga

nzolekana kutali ndi zochita zanu,

ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

10 2Ako. 9.10 “Mvula ndi chisanu chambee

zimatsika kuchokera kumwamba,

ndipo sizibwerera komweko,

koma zimathirira nthaka.

Zimameretsa ndi kukulitsa zomera,

kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya.

11Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga.

Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake,

koma adzachita zonse zimene ndifuna,

ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino.

12“Inu anthu anga,

mudzachoka ku Babiloni mokondwa,

adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere.

Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo.

Nayonso mitengo yonse yam'thengo

idzakuwomberani m'manja.

13Kumene tsopano kuli mitengo yaminga

kudzamera mitengo ya paini.

Kumene tsopano kuli mkandankhuku kudzamera michisu.

Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Ine Chauta,

ngati chizindikiro chamuyaya

chimene sichidzafafanizika konse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help