1Usiku uliwonse ndili gone pabedi panga
ndinkangomufunafuna amene mtima wanga umamkonda.
Ndidamufunafuna koma osampeza.
Ndidamuitana, koma iye osandiyankha.
2Ndiye ndidati,
“Ai, tsopano ndidzuka ndi kuloŵa mu mzinda,
m'miseu ndi m'mabwalo.
Ndimufunafuna amene mtima wanga umamkonda.”
Ndidamufunafunadi, koma osampeza.
3Alonda adandipeza
pamene ankayendera mzinda.
Ndidaŵafunsa kuti,
“Kodi mwandiwonerako amene mtima wanga umamkonda?”
4Ndidangoti iwo aja ntaŵapitirira pang'ono,
ndampeza amene mtima wanga umamkonda.
Ndidamgwira, osamlola kuti achoke,
mpaka nditamloŵetsa m'nyumba ya amai anga,
m'chipinda cha amene adandibala.
5Inu akazi a ku Yerusalemu,
ndithu ndakupembani,
pali mphoyo ndi nswala zakuthengo,
chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa
mpaka pamene chifunire ichocho.
Nyimbo Yachitatu.Mkazi
6Kodi nchiyaninso icho
chikutulukira ku chipululucho
ngati utsi watolotolo,
chonunkhira mure ndi lubani,
chokhala ndi zonunkhira zonse
zogulitsa anthu amalonda?
7Amenewo ndi machira a Solomoni.
Pali ankhondo makumi asanu ndi limodzi,
amuna anyonga a ku Israele operekeza.
8Onsewo agwira malupanga,
ndipo ngodziŵa kumenya nkhondo,
aliyense wavala lupanga pambali pake,
kuti alimbane ndi aupandu usiku.
9Mfumu Solomoni adadzipangira machira
a matabwa a ku Lebanoni.
10Milongoti yake adapanga yasiliva,
kumbuyo kwake kunali kwagolide,
pampando pake panali nsalu yofiirira.
11Tulukani, inu akazi a ku Ziyoni,
mudzaone Mfumu Solomoni,
atavala chisoti chaufumu
chimene mai wake adamuveka
pa tsiku la ukwati wake,
tsiku limene mtima wake unkasangalala.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.