Rut. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Rute apeza mwamuna.

1Tsiku lina Naomi adafunsa Rute kuti, “Kodi iwe mwana wanga, nanga sikwabwino kuti ndikupezere pokhala, kuti zinthu zizikuyendera bwino?

2Bowazi amene adzakazi ake unali nawo, ndi wachibale wathu. Usiku uno iye akhala akupuntha barele ku malo ake opunthira.

3Samba tsono, udzole mafuta ndipo uvale zovala zabwino kwambiri, upite kopunthirako. Koma munthuyo asakakuzindikire mpaka atamaliza kudya ndi kumwa.

4Pamene akukagona, ukaonetsetse malo amene akagonewo. Tsono ukavundukule chofunda chake nukagona ku mapazi ake. Motero iyeyo akakuuza zoti uchite.”

5Rute adayankha kuti, “Zonse mwanenazi ndichita.”

6Choncho Rute adapita kopunthira kuja, ndipo adakachitadi monga momwe mpongozi wake uja adaamuuzira.

7Bowazi atamaliza kudya ndi kumwa, anali wosangalala, ndipo adapita kukagona pambali pa mulu wa barele. Tsono Rute adabwera mopanda mtswatswa, adavundukula mapazi a Bowazi, nagona pomwepo.

8Tsono pakati pa usiku Bowazi adadzidzimuka natembenuka, naona mkazi atagona ku mapazi ake. Adafunsa kuti, “Ndiwe yani?”

9Mkaziyo adayankha kuti, “Ndine Rute mdzakazi wanu. Popeza kuti ndinu wachibale, muyenera kundiwombola pakundiloŵa chokolo.”

10Apo Bowazi adati, “Chauta akudalitse, mwana wanga. Zabwino wachita potsirizazi zikupambana zoyamba zija zimene udachitira mpongozi wako, poti sudapite kwa anyamata osauka kapena olemera.

11Tsopano usadandaule, mwana wanga. Ndidzakuchitira zonse zimene upemphe, pakuti anzanga am'mudzimu akudziŵa kuti ndiwe mkazi wabwino.

12Rut. 2.20 Nzoona, ine ndine wachibale, komabe alipo wachibale weniweni kupambana ine.

13Gona konkuno usiku uno mpaka m'maŵa. Ngati iyeyo adzakuloŵe chokolo, chabwino aloŵe. Koma ngati safuna, ndidzakuloŵa ndine, ndikulumbira pamaso pa Chauta wamoyo. Gona mpaka m'maŵa.”

14Choncho Rute adagona ku mapazi a Bowazi mpaka m'maŵa, koma adadzuka kudakali kamdimabe, chifukwa Bowaziyo sankafuna kuti anthu adziŵe kuti mkaziyo adaabwera kopunthira bareleko.

15Tsono Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho, uchiyale pansi.” Rute adayala chofundacho, ndipo Bowazi adayesa makilogramu makumi aŵiri a barele, namsenzetsa Rute uja. Tsono Rute adachoka nakaloŵa mu mzinda.

16Atafika kwa mpongozi wake uja, mpongoziyo adati, “Zinthu zakuyendera bwanji, mwana wanga?” Rute adamfotokozera zonse zimene munthu uja adamchitira,

17ndipo adati, “Wandipatsa makilogramu makumi aŵiri a barele, nandiwuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’ ”

18Apongozi akewo adayankha kuti, “Dikira mwana wanga, tiwone m'mene zikhalire zinthu, chifukwa munthuyo salekera pomwepo, koma azikonza zimenezi lero.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help